Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 3:14

[1] Nʼchifukwa chiyani Yehova mwayima patali? Chifukwa chiyani mukudzibisa nokha pa nthawi ya mavuto?

[2] Mwa kunyada kwake munthu woyipa asaka wofowoka, amene akodwa mʼnjira zimene iye wakonza.

[3] Iye amatamandira zokhumba za mu mtima wake; amadalitsa aumbombo ndi kuchitira chipongwe Yehova.

[4] Mwa kunyada kwake woyipa safunafuna Mulungu; mʼmaganizo ake wonse mulibe malo a Mulungu.

[5] Zinthu zake zimamuyendera bwino; iye ndi wamwano ndipo malamulo anu ali nawo kutali; amanyogodola adani ake onse.

[6] Iye amadziyankhulira kuti, “Palibe chimene chidzandigwedeze. Ndidzakhala wokondwa nthawi zonse ndipo sindidzakhala pa mavuto.”

[7] Mʼkamwa mwake mwadzaza matemberero, mabodza ndi zoopseza; zovutitsa ndi zoyipa zili pansi pa lilime lake.

[8] Iye amabisalira anthu pafupi ndi midzi, kuchokera pobisalapo amapha anthu osalakwa, amayangʼanayangʼana mwachinsinsi anthu oti awawononge.

[9] Amabisalira anthu ngati mkango pa zitsamba. Amabisalira kuti agwire anthu opanda mphamvu; amagwira anthu opanda mphamvu ndi kuwakokera mu ukonde wake.

[10] Anthuwo amawapondaponda ndipo amakomoka; amakhala pansi pa mphamvu zake.

[11] Iye amati mu mtima mwake, “Mulungu wayiwala, wabisa nkhope yake ndipo sakuonanso.”

[12] Dzukani Yehova! Onetsani dzanja lanu Inu Mulungu. Musayiwale anthu opanda mphamvu.

[13] Nʼchifukwa chiyani munthu woyipa amachitira chipongwe Mulungu? Chifukwa chiyani amati mu mtima mwake, “Iye sandiyimba mlandu?”

[14] Komatu Inu Mulungu, mumazindikira mavuto ndi zosautsa, mumaganizira zochitapo kanthu. Wovutikayo amadzipereka yekha kwa Inu pakuti Inu ndi mthandizi wa ana amasiye.

[15] Thyolani dzanja la woyipitsitsa ndi la munthu woyipa; muzengeni mlandu chifukwa cha zoyipa zake zimene sizikanadziwika.

[16] Yehova ndi Mfumu kwamuyaya; mitundu ya anthu idzawonongeka kuchoka mʼdziko lake.

[17] Mumamva Inu Yehova, zokhumba za osautsidwa; mumawalimbikitsa ndipo mumamva kulira kwawo.

[18] Kuteteza ana amasiye ndi oponderezedwa, ndi cholinga chakuti munthu amene ali wa dziko lapansi asaopsenso.

Masalimo — Chapters