Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 2:03

[1] Nʼchifukwa chiyani anthu a mitundu ina akufuna kuchita chiwembu? Akonzekeranji zopanda pake anthu?

[2] Mafumu a dziko lapansi akugwirizana nazo; ndipo olamulira asonkhana pamodzi kulimbana ndi Ambuye ndi wodzozedwa wakeyo.

[3] Iwo akunena kuti, “Tiyeni timasule magoli awo ndipo titaye zingwe zawo.”

[4] Wokhala mmwamba akuseka; Ambuye akuwanyoza iwowo.

[5] Ndipo iye awadzudzula mu mkwiyo wake ndi kuwaopseza mu ukali wake, kunena kuti,

[6] “Ine ndakhazikitsa mfumu yanga pa Ziyoni, phiri langa loyera.”

[7] Ine ndidzalengeza zimene Yehova walamula: Iye anati kwa Ine, “Iwe ndiwe mwana wanga; lero Ine ndakhala Atate ako.

[8] Tandipempha, ndipo ndidzachititsa kuti mitundu ya anthu ikhale cholowa chako; malekezero a dziko lapansi kuti akhale chuma chako.

[9] Iweyo udzawalamulira ndi ndodo yaufumu yachitsulo; udzawaphwanya zidutswazidutswa ngati zowumba zadothi.”

[10] Kotero, inu mafumu, chenjerani; chenjezedwani, inu olamulira a dziko lapansi.

[11] Tumikirani Yehova mwa mantha ndi kukondwerera ulamuliro wake monjenjemera.

[12] Mpsopsoneni mwanayo kuti angakwiye; kuti mungawonongedwe mʼnjira zanu, pakuti ukali wake utha kuuka mʼkanthawi kochepa. Odala ndi onse amene amathawira kwa Iye.

Masalimo — Chapters