Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 3:10

[1] Mundichitire chifundo, Inu Mulungu, molingana ndi chikondi chanu chosasinthika; molingana ndi chifundo chanu chachikulu mufafanize mphulupulu zanga.

[2] Munditsuke zolakwa zanga zonse ndipo mundiyeretse kuchotsa tchimo langa.

[3] Pakuti ndikudziwa mphulupulu zanga, ndipo tchimo langa lili pamaso panga nthawi zonse.

[4] Motsutsana ndi Inu, Inu nokha, ndachimwa ndipo ndachita zoyipa pamaso panu, Kotero kuti inu mwapezeka kuti ndinu wolungama pamene muyankhula ndi pamene muweruza.

[5] Zoonadi ine ndinali wochimwa pomwe ndimabadwa, wochimwa kuyambira pa nthawi imene amayi anga anakhala woyembekezera ine.

[6] Zoonadi inu mumafuna choonadi mu ziwalo zamʼkati mwanga; mumandiphunzitsa nzeru mʼkati mwanga mwenimweni.

[7] Mundiyeretse ndi hisope ndipo ndidzayera, munditsuke ndipo ndidzayera kuposa matalala

[8] Mundilole ndimve chimwemwe ndi chisangalalo, mulole kuti mafupa amene mwawamphwanya akondwere.

[9] Mufulatire machimo anga ndi kufafaniza zolakwa zanga zonse.

[10] Mulenge mʼkati mwanga mtima woyera Inu Mulungu ndi kukonzanso mzimu wokhazikika mwa ine.

[11] Musandichotse pamaso panu kapena kuchotsa Mzimu wanu Woyera mwa ine.

[12] Bwezeretsani mwa ine chimwemwe cha chipulumutso chanu ndipo mundipatse mzimu wofuna kumvera kuti undilimbitse.

[13] Pamenepo ndidzaphunzitsa anthu amphulupulu njira zanu kuti ochimwa adzabwerere kwa inu.

[14] Mundipulumutse ku tchimo lokhetsa magazi, Inu Mulungu, Mulungu wa chipulumutso changa, ndipo lilime langa lidzayimba zachilungamo chanu.

[15] Inu Ambuye tsekulani milomo yanga, ndipo pakamwa panga padzalengeza matamando anu.

[16] Inu simusangalatsidwa ndi nsembe wamba. Ndikanapereka nsembe yopsereza, Inu simukondwera nayo.

[17] Nsembe za Mulungu ndi mzimu wosweka; mtima wosweka ndi wachisoni Inu Mulungu simudzawunyoza.

[18] Mwa kukoma mtima kwanu mupange Ziyoni kuti alemere; mumange makoma a Yerusalemu.

[19] Kotero kudzakhala nsembe zachilungamo, nsembe yonse yopsereza yokondweretsa Inu; ndipo ngʼombe zazimuna zidzaperekedwa pa guwa lanu la nsembe.

Masalimo — Chapters