Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 1:32

[1] Tamandani Yehova. Ndidzathokoza Yehova ndi mtima wanga wonse mʼbwalo la anthu olungama mtima ndi pa msonkhano.

[2] Ntchito za Yehova nʼzazikulu; onse amene amakondwera nazo amazilingalira.

[3] Zochita zake ndi za ulemerero ndi zaufumu, ndipo chilungamo chake ndi chosatha.

[4] Iye wachititsa kuti zodabwitsa zake zikumbukirike; Yehova ndi wokoma mtima ndi wachifundo.

[5] Amapereka chakudya kwa amene amamuopa Iye; amakumbukira pangano lake kwamuyaya.

[6] Waonetsa anthu ake mphamvu ya ntchito zake, kuwapatsa mayiko a anthu a mitundu ina.

[7] Ntchito za manja ake ndi zokhulupirika ndi zolungama; malangizo ake onse ndi odalirika.

[8] Malamulo ndi okhazikika ku nthawi za nthawi, ochitidwa mokhulupirika ndi molungama.

[9] Iyeyo amawombola anthu ake; anakhazikitsa pangano lake kwamuyaya dzina lake ndi loyera ndi loopsa.

[10] Kuopa Yehova ndicho chiyambi cha nzeru; onse amene amatsatira malangizo ake amamvetsa bwino zinthu. Iye ndi wotamandika mpaka muyaya.

Masalimo — Chapters