Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 2:59

[1] Ndidzayamika Yehova nthawi zonse; matamando ake adzakhala pa milomo yanga nthawi zonse.

[2] Moyo wanga udzanyadira Yehova; anthu osautsidwa amve ndi kukondwera.

[3] Lemekezani Yehova pamodzi ndi ine; tiyeni pamodzi tikuze dzina lake.

[4] Ine ndinafunafuna Yehova ndipo Iye anandiyankha; anandilanditsa ku mantha anga onse.

[5] Iwo amene amayangʼana kwa Iye, nkhope zawo zimanyezimira; nkhope zawo sizikhala zophimbidwa ndi manyazi.

[6] Munthu wosauka uno anayitana, ndipo Yehova anamumva; Yehova anamupulumutsa ku mavuto ake onse.

[7] Mngelo wa Yehova amatchinjiriza amene amakonda Iye ndi kuwalanditsa.

[8] Lawani ndipo onani kuti Yehova ndi wabwino; wodala munthu amene amathawira kwa Iye.

[9] Wopani Yehova inu oyera mtima ake, pakuti iwo amene amaopa Iye sasowa kanthu.

[10] Mikango itha kulefuka ndi kumva njala koma iwo amene amafunafuna Yehova sasowa kanthu kalikonse kabwino.

[11] Bwerani ana anga, mundimvere; ndidzakuphunzitsani kuopa Yehova.

[12] Aliyense wa inu amene amakonda moyo wake ndi kukhumba kuti aone masiku abwino ambiri,

[13] asunge lilime lake ku zoyipa ndi milomo yake kuti isayankhule zonama.

[14] Tembenuka kuchoka ku zoyipa ndipo chita zabwino; funafuna mtendere ndi kuwulondola.

[15] Maso a Yehova ali pa olungama ndipo makutu ake ali tcheru kumva kulira kwawo;

[16] nkhope ya Yehova ikutsutsana ndi amene amachita zoyipa, kuwachotsa kuti asawakumbukirenso pa dziko lapansi.

[17] Olungama amafuwula, ndipo Yehova amawamva; Iye amawalanditsa ku mavuto awo onse.

[18] Yehova ali pafupi kwa osweka mtima ndipo amapulumutsa iwo amene asweka mu mzimu.

[19] Munthu wolungama atha kukhala ndi mavuto ambiri, Koma Yehova amamulanditsa ku mavuto onsewo,

[20] Iye amateteza mafupa ake onse, palibe limodzi la mafupawo limene lidzathyoledwa.

[21] Choyipa chidzapha anthu oyipa; adani a olungama adzapezeka olakwa.

[22] Yehova amawombola atumiki ake; aliyense amene amathawira kwa Iye sadzapezeka wolakwa.

Masalimo — Chapters