Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 1:16

[1] Mwa Yehova ine ndimathawiramo. Nanga mungathe bwanji kunena kwa ine kuti, “Thawira ku phiri lako ngati mbalame.

[2] Pakuti taona oyipa akunga mauta awo; ayika bwino mivi yawo pa zingwe za uta, pobisala pawo kuti alase olungama mtima.

[3] Tsono ngati maziko awonongeka, olungama angachite chiyani?”

[4] Yehova ali mʼNyumba yake yoyera; Yehova ali pa mpando wake waufumu kumwamba. Iye amayangʼanitsitsa ana a anthu; maso ake amawayesa.

[5] Yehova amayesa olungama, koma moyo wake umadana ndi oyipa, amene amakonda zachiwawa.

[6] Iye adzakhuthulira pa oyipa makala amoto ndi sulufule woyaka; mphepo yotentha idzakhala yowayenera.

[7] Pakuti Yehova ndi wolungama, Iye amakonda chilungamo; ndipo anthu olungama adzaona nkhope yake.

Masalimo — Chapters