Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 2:25

[1] Inu Mulungu musakhale chete; musangoti phee, Mulungu musangoti duu.

[2] Onani adani anu akuchita chiwawa, amene amadana nanu autsa mitu yawo.

[3] Mochenjera iwo akukambirana za chiwembu kutsutsana ndi anthu anu; Iwo akukonzekera kutsutsana ndi omwe mumawakonda.

[4] Iwo akunena kuti, “Bwerani” akutero, “Tiyeni tiwononge mtundu wonsewu kuti dzina la Israeli lisakumbukikenso.”

[5] Ndi mtima umodzi akukonzekera chiwembu; Iwo achita mgwirizano kutsutsana nanu:

[6] Matenti a Edomu ndi Aismaeli, Mowabu ndi Ahagiri,

[7] Agebala, Aamoni ndi Aamaleki, Afilisti, pamodzi ndi anthu a ku Turo.

[8] Ngakhalenso Aasiriya aphatikizana nawo kupereka mphamvu kwa ana a Loti. q4 Sela

[9] Muwachitire zomwe munachitira Amidiyani, monga munachitira Sisera ndi Yabini ku mtsinje wa Kisoni.

[10] Amene anawonongedwa ku Endori ndi kukhala ngati zinyalala.

[11] Anthu awo otchuka muwachite zomwe munachita Orebu ndi Zeebu ana a mafumu muwachite zomwe munachita Zeba ndi Zalimuna,

[12] amene anati, “Tiyeni tilande dziko la msipu la Mulungu.”

[13] Muwasandutse fumbi lowuluka, Inu Mulungu wanga, ngati mankhusu owuluka ndi mphepo.

[14] Monga moto umatentha nkhalango, kapena malawi a moto kuyatsa phiri,

[15] kotero muwathamangitse ndi mphepo yamkuntho, ndi kuwachititsa mantha ndi namondwe.

[16] Muphimbe nkhope zawo ndi manyazi kuti adzafunefune dzina lanu Yehova.

[17] Achite manyazi ndi mantha nthawi zonse; awonongeke mwa manyazi.

[18] Adziwe kuti Inu amene dzina lanu ndi Yehova, ndinu nokha Wammwambamwamba pa dziko lonse lapansi.

Masalimo — Chapters