Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 1:33

[1] Perekani kwa Yehova, inu anthu amphamvu, perekani kwa Yehova ulemerero ndi mphamvu.

[2] Perekani kwa Yehova ulemerero woyenera dzina lake, pembedzani Yehova mwa kukongola kwa chiyero chake.

[3] Liwu la Yehova lili pamwamba pa madzi; Mulungu waulemerero abangula, Yehova abangula pamwamba pa madzi amphamvu.

[4] Liwu la Yehova ndi lamphamvu; liwu la Yehova ndi laulemerero.

[5] Liwu la Yehova limathyola mikungudza; Yehova amathyolathyola mikungudza ya ku Lebanoni.

[6] Iye amachititsa Lebanoni kulumphalumpha ngati mwana wangʼombe, Siriyoni ngati mwana wa njati:

[7] Liwu la Yehova limakantha ngati kungʼanima kwa mphenzi.

[8] Liwu la Yehova limagwedeza chipululu; Yehova amagwedeza chipululu cha Kadesi.

[9] Liwu la Yehova limapindapinda mibawa ndi kuyeretsa nkhalango. Ndipo mʼNyumba mwake onse amafuwula kuti, “Ulemerero!”

[10] Yehova amakhala pamwamba pa madzi osefukira, Yehova ndiye mfumu kwamuyaya.

[11] Yehova amapereka mphamvu kwa anthu ake; Yehova amadalitsa anthu ake ndi mtendere.

Masalimo — Chapters