Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 0:51

[1] Akanapanda kukhala mbali yathu Yehova, anene tsono Israeli,

[2] akanapanda kukhala mbali yathu Yehova, potiwukira anthuwo,

[3] iwo atatipsera mtima, akanatimeza amoyo;

[4] chigumula chikanatimiza, mtsinje ukanatikokolola,

[5] madzi a mkokomo akanatikokolola.

[6] Atamandike Yehova, amene sanalole kuti tikhale chakudya cha mano awo.

[7] Moyo wathu wawonjoka ngati mbalame yokodwa mu msampha wa mlenje; msampha wathyoka, ndipo ife tapulumuka.

[8] Thandizo lathu lili mʼdzina la Yehova wolenga kumwamba ndi dziko lapansi.

Masalimo — Chapters