Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 3:00

[1] Inu Yehova Mulungu wanga, Ine ndikuthawira kwa Inu; pulumutseni ndi kundilanditsa kwa onse amene akundithamangitsa,

[2] mwina angandikadzule ngati mkango, ndi kundingʼamba popanda wondipulumutsa.

[3] Inu Yehova Mulungu wanga, ngati ndachita izi ndipo ndapezeka wolakwa,

[4] ngati ndachita zoyipa kwa iye amene ndili naye pa mtendere, kapena popanda chifukwa ndalanda mdani wanga,

[5] pamenepo lolani adani anga andithamangitse ndi kundipitirira, lolani kuti moyo wanga aupondereze pansi ndipo mundigoneke pa fumbi. q4 Sela

[6] Nyamukani Yehova, mu mkwiyo wanu; nyamukani kutsutsana ndi mkwiyo wa adani anga. Dzukani Mulungu wanga, lamulirani chilungamo chanu.

[7] Lolani gulu la anthu a mitundu ina lisonkhane mokuzungulirani. Alamulireni muli kumwambako;

[8] Yehova aweruzeni anthu a mitundu inayo. Ndiweruzeni Yehova, monga mwa chilungamo changa, monga mwa moyo wanga wangwiro, Inu Wammwambamwamba.

[9] Inu Mulungu wolungama, amene mumasanthula maganizo ndi mitima, thetsani chiwawa cha anthu oyipa ndipo wolungama akhale motetezedwa.

[10] Chishango changa ndi Mulungu Wammwambamwamba, amene amapulumutsa olungama mtima.

[11] Mulungu amaweruza molungama, Mulungu amene amaonetsa ukali wake tsiku ndi tsiku.

[12] Ngati munthu satembenuka, Mulungu adzanola lupanga lake, Iye adzawerama ndi kukoka uta.

[13] Mulungu wakonza zida zake zoopsa; Iye wakonzekera mivi yake yoyaka moto.

[14] Taonani, munthu woyipa amalingalira zoyipa zokhazokha nthawi zonse. Zochita zake ndi zosokoneza ndi zovutitsa anthu ena.

[15] Iye amene akumba dzenje ndi kulizamitsa amagwera mʼdzenje limene wakumbalo.

[16] Mavuto amene amayambitsa amamubwerera mwini; chiwawa chake chimatsikira pa mutu wake womwe.

[17] Ine ndidzayamika Yehova chifukwa cha chilungamo chake; ndipo ndidzayimba nyimbo zamatamando pa dzina la Yehova Wammwambamwamba.

Masalimo — Chapters