[1] Mʼmbali mwa mitsinje ya ku Babuloni tinakhala pansi ndi kulira pamene tinakumbukira Ziyoni.
[2] Kumeneko, pa mitengo ya misondozi tinapachika apangwe athu,
[3] pakuti anthu otigwira ukapolo anatipempha kuti tiyimbe nyimbo. Otizunza athu anafuna nyimbo zachisangalalo; iwo anati, “Tiyimbireni imodzi mwa nyimbo za ku Ziyoni!”
[4] Tingayimbe bwanji nyimbo za Yehova mʼdziko lachilendo?
[5] Ndikakuyiwala iwe Yerusalemu, dzanja langa lamanja liyiwale luso lake.
[6] Lilime langa limamatire ku nkhama za mʼkamwa mwanga ndikapanda kukukumbukira iwe Yerusalemu, ngati sindiyesa iwe chimwemwe changa chachikulu.
[7] Kumbukirani, Inu Yehova, zimene Aedomu anachita pa tsiku limene Yerusalemu anagonja. Iwowo anafuwula kuti, “Mugwetseni pansi, mugwetseni pansi mpaka pa maziko ake!”
[8] Iwe mwana wa mkazi wa Babuloni, woyenera kuwonongedwa, wodalitsika ndi yemwe adzakubwezera pa zimene watichitira.
[9] Amene adzagwira makanda ako ndi kuwakankhanthitsa pa miyala.