Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 1:11

[1] Ndinakondwera atandiwuza kuti, “Tiyeni ku nyumba ya Yehova.”

[2] Mapazi athu akuyima mʼzipata zako, Iwe Yerusalemu.

[3] Yerusalemu anamangidwa ngati mzinda umene uli wothithikana pamodzi.

[4] Kumeneko ndiye kumene kumapita mafuko, mafuko a Yehova, umboni wa kwa Israeli, kuti atamande dzina la Yehova.

[5] Kumeneko anayikako mipando yaufumu yachiweruzo, mipando yaufumu ya nyumba ya Davide.

[6] Pemphererani mtendere wa Yerusalemu: “Iwo amene amakukonda iwe zinthu ziwayendere bwino.

[7] Mukhale mtendere mʼkati mwa makoma ako, ndipo mʼnyumba zako zaufumu mukhale chitetezo.”

[8] Chifukwa cha abale anga ndi abwenzi anga ndidzati, “Mtendere ukhale mʼkati mwako.”

[9] Chifukwa cha Nyumba ya Yehova Mulungu wathu, ndidzakufunira zabwino.

Masalimo — Chapters