Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 1:21

[1] Thandizeni Yehova pakuti palibe munthu wokhulupirika; okhulupirika akusowa pakati pa anthu.

[2] Aliyense amanamiza mʼbale wake; ndi pakamwa pawo pabodza amayankhula zachinyengo.

[3] Inu Yehova tsekani milomo yonse yachinyengo ndi pakamwa paliponse podzikuza.

[4] Pakamwa pamene pamati, “Ife tidzapambana ndi kuyankhula kwathu; pakamwapa ndi pathupathu, tsono mbuye wathu ndani?”

[5] “Chifukwa cha kuponderezedwa kwa anthu opanda mphamvu ndi kubuwula kwa anthu osowa, Ine ndidzauka tsopano,” akutero Yehova, “Ndidzawateteza kwa owazunza.”

[6] Ndipo mawu a Yehova ndi angwiro monga siliva oyengedwa mʼngʼanjo yadothi, oyengedwa kasanu nʼkawiri.

[7] Inu Yehova mudzatitchinjiriza ndipo mudzatiteteza kwa anthu otere kwamuyaya.

[8] Oyipa amangoyendayenda ponseponse anthu akamayamikira zochita zawo.

Masalimo — Chapters