Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 1:14

[1] Imvani kulira kwanga, Inu Mulungu; mvetserani pemphero langa.

[2] Kuchokera ku malekezero a dziko lapansi ine ndimayitana Inu ndimayitana pomwe mtima wanga ukufowoka; tsogolereni ku thanthwe lalitali kuposa ineyo.

[3] Pakuti Inu mwakhala pothawirapo panga, nsanja yolimba polimbana ndi adani anga.

[4] Ine ndikulakalaka kukhala mʼtenti yanu kwamuyaya ndi kupeza chitetezo mu mthunzi wa mapiko anu.

[5] Pakuti Inu Mulungu mwamva malumbiro anga; mwandipatsa cholowa cha iwo amene amaopa dzina lanu.

[6] Wonjezerani masiku a moyo wa mfumu, zaka zake kwa mibado yochuluka.

[7] Iye akhale pa mpando waufumu pamaso pa Mulungu kwamuyaya; ikani chikondi chanu ndi kukhulupirika kwanu kuti zimuteteze.

[8] Kotero ndidzayimba matamando kwamuyaya pa dzina lanu ndi kukwaniritsa malumbiro anga tsiku ndi tsiku.

Masalimo — Chapters