Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 1:20

[1] Yehova akuwuza Mbuye wanga kuti, “Khala ku dzanja langa lamanja mpaka nditasandutsa adani ako kukhala chopondapo mapazi ako.”

[2] Yehova adzakuza ndodo yamphamvu ya ufumu wako kuchokera mʼZiyoni; udzalamulira pakati pa adani ako.

[3] Ankhondo ako adzakhala odzipereka pa tsiku lako la nkhondo. Atavala chiyero chaulemerero, kuchokera mʼmimba ya mʼbandakucha, udzalandira mame a unyamata wako.

[4] Yehova walumbira ndipo sadzasintha maganizo ake: “Ndiwe wansembe mpaka muyaya monga mwa unsembe wa Melikizedeki.”

[5] Ambuye ali kudzanja lako lamanja; Iye adzaponda mafumu pa tsiku la ukali wake.

[6] Adzaweruza anthu a mitundu ina, adzadzaza dziko lapansi ndi mitembo ndipo adzaphwanya olamulira a pa dziko lonse lapansi.

[7] Iye adzamwa mu mtsinje wa mʼmbali mwa njira; choncho adzaweramutsa mutu wake.

Masalimo — Chapters