Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 1:44

[1] Inu Yehova ndikukuyitanani; bwerani msanga kwa ine. Imvani mawu anga pamene ndiyitana Inu.

[2] Pemphero langa lifike kwa Inu ngati lubani; kukweza manja kwanga kukhale ngati nsembe yamadzulo.

[3] Yehova ikani mlonda pakamwa panga; londerani khomo la pa milomo yanga.

[4] Musalole kuti mtima wanga ukokedwere ku zoyipa; kuchita ntchito zonyansa pamodzi ndi anthu amene amachita zoyipa; musalole kuti ndidye nawo zokoma zawo.

[5] Munthu wolungama andikanthe, chimenecho ndiye chifundo; andidzudzule ndiye mafuta pa mutu wanga. Mutu wanga sudzakana zimenezi. Komabe pemphero langa nthawi zonse ndi lotsutsana ndi ntchito za anthu ochita zoyipa.

[6] Olamulira awo adzaponyedwa pansi kuchokera pa malo okwera kwambiri, ndipo anthu oyipa adzaphunzira kuti mawu anga anayankhulidwa bwino.

[7] Iwo adzati, “Monga momwe nkhuni zimamwazikira akaziwaza, ndi momwenso mafupa athu amwazikira pa khomo la manda.”

[8] Koma maso anga akupenyetsetsa Inu Ambuye Wamphamvuzonse; ndimathawira kwa Inu, musandipereke ku imfa.

[9] Mundipulumutse ku misampha imene anditchera, ku makhwekhwe amene anthu oyipa andikonzera.

[10] Anthu oyipa akodwe mʼmaukonde awo, mpaka ine nditadutsa mwamtendere.

Masalimo — Chapters