Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 1:23

[1] Chitsiru chimati mu mtima mwake, “Kulibe Mulungu.” Oterewa ndi oyipa ndipo ntchito zawo ndi zonyansa; palibe amene amachita zabwino.

[2] Yehova kumwamba wayangʼana pansi, kuyangʼana anthu onse kuti aone ngati alipo wina wanzeru, amene amafunafuna Mulungu.

[3] Onse atembenukira kumbali, onse pamodzi asanduka oyipa; palibe amene amachita zabwino, palibiretu ndi mmodzi yemwe.

[4] Kodi anthu ochita zoyipawa sadziwa chilichonse? Akudya anthu anga ngati chakudya chawo ndipo satamanda Yehova?

[5] Awo ali apowo, agwidwa ndi mantha aakulu, pakuti Mulungu ali mʼgulu la olungama.

[6] Inu ochita zoyipa mumalepheretsa chikonzero cha anthu osauka, koma Yehova ndiye pothawirapo pawo.

[7] Ndithu, chipulumutso cha Israeli chidzachokera ku Ziyoni! Pamene Yehova abwezeretsa ufulu wa anthu ake, Yakobo akondwere ndipo Israeli asangalale!

Masalimo — Chapters