Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 1:28

[1] Tamandani Yehova. Tamanda Yehova, iwe moyo wanga.

[2] Ndidzatamanda Yehova ndi moyo wanga wonse; ndidzayimba nyimbo zamatamando kwa Mulungu wanga nthawi yonse ya moyo wanga.

[3] Musamadalire mafumu, anthu osakhalitsa, amene sangathe kupulumutsa.

[4] Pamene mizimu yawo yachoka, iwo amabwerera ku dothi; zimene ankafuna kuchita zimatha tsiku lomwelo.

[5] Wodala ndi amene thandizo lake ndi Mulungu wa Yakobo.

[6] Wolenga kumwamba ndi dziko lapansi, nyanja ndi zonse zili mʼmenemo; Yehova, amene ndi wokhulupirika kwamuyaya.

[7] Iye amachitira chilungamo anthu oponderezedwa ndipo amapereka chakudya kwa anthu anjala. Yehova amamasula amʼndende,

[8] Yehova amatsekula maso anthu osaona, Yehova amadzutsa onse amene awerama pansi, Yehova amakonda anthu olungama.

[9] Yehova amasamalira alendo ndipo amathandiza ana ndi akazi amasiye, koma amasokoneza njira za anthu oyipa.

[10] Yehova ndiye Mfumu mpaka muyaya, Mulungu wako iwe Ziyoni, pa mibado yonse. Tamandani Yehova.

Masalimo — Chapters