Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 2:06

[1] Landitseni Yehova kwa anthu oyipa; tetezeni kwa anthu ankhanza,

[2] amene mu mtima mwawo amakonza zinthu zoyipa ndi kuyambitsa nkhondo tsiku lililonse.

[3] Iwo amanola malilime awo kukhala akuthwa ngati a njoka; pa milomo yawo pali ululu wa mamba. q4 Sela

[4] Tetezeni Inu Yehova, kwa anthu oyipa; tchinjirizeni kwa anthu ankhanza amene amakonza zokola mapazi anga.

[5] Anthu odzikuza anditchera msampha mobisika; iwo atchera zingwe za maukonde awo ndipo anditchera misampha pa njira yanga. q4 Sela

[6] Inu Yehova, ine ndikuti, “Ndinu Mulungu wanga.” Imvani kupempha kwanga Yehova.

[7] Inu Ambuye Wamphamvuzonse, Mpulumutsi wanga wamphamvu, mumateteza mutu wanga tsiku lankhondo.

[8] Musawapatse anthu oyipa zokhumba zawo, Inu Yehova; musalole kuti zokonza zawo zitheke, mwina iwo adzayamba kunyada. q4 Sela

[9] Mitu ya amene andizungulira iphimbidwe ndi masautso amene milomo yawo yayambitsa.

[10] Makala amoto agwere pa iwo; aponyedwe pa moto, mʼmaenje amatope, asatulukemonso.

[11] Musalole kuti anthu achipongwe akhazikike mʼdziko; choyipa chilondole anthu ankhanza.

[12] Ndikudziwa kuti Yehova amapereka chiweruzo cholungama kwa anthu osauka, ndipo amateteza zolinga za anthu osowa.

[13] Zoonadi anthu olungama adzatamanda dzina lanu, ndipo anthu owongoka mtima adzakhala pamaso panu.

Masalimo — Chapters