Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 1:25

[1] Yehova akuyankhe pamene uli pa msautso; dzina la Mulungu wa Yakobo likuteteze.

[2] Iye atumize thandizo kuchokera ku malo ake opatulika; akugwirizize kuchokera ku Ziyoni.

[3] Iye akumbukire nsembe zako zonse ndipo alandire nsembe zako zopsereza. q4 Sela

[4] Akupatse chokhumba cha mtima wako ndipo akuthandize kuti zonse wakonza zichitike.

[5] Ife tidzafuwula ndi chimwemwe pamene iwe wapambana ndipo tidzanyamula mbendera zathu mʼdzina la Mulungu wathu, Yehova ayankhe zopempha zako zonse.

[6] Tsopano ndadziwa kuti Yehova amapulumutsa wodzozedwa wake; Iye amamuyankha kuchokera kumwamba ku malo ake opatulika ndi mphamvu yopulumutsa ya dzanja lake lamanja.

[7] Ena amadalira magaleta ndipo ena akavalo koma ife tidzadalira dzina la Yehova Mulungu wathu.

[8] Iwo amagonjetsedwa ndi kugwa, koma ife timadzuka ndi kuyima chilili.

[9] Inu Yehova, pulumutsani mfumu! Tiyankheni pamene tikuyitanani!

Masalimo — Chapters