Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 1:58

[1] Wodala ndi munthu amene amaganizira anthu osauka; Yehova amamuwombola pa nthawi yamsautso.

[2] Yehova adzamuteteza ndi kusunga moyo wake; Yehova adzamudalitsa iye mʼdziko ndipo sadzamupereka ku zofuna za adani ake.

[3] Yehova adzamuthandiza pamene akudwala ndipo adzamuchiritsa pa bedi lake la matenda.

[4] Ndinati, “Inu Yehova, mundichitire chifundo; chiritseni pakuti ndakuchimwirani.”

[5] Adani anga mwankhwidzi amanena za ine kuti, “Kodi munthu ameneyu adzafa liti kuti ayiwalike?”

[6] Pamene wina abwera kudzandiona, amayankhula mwachinyengo, pomwe mtima wake ukusonkhanitsa zachipongwe; kenaka iye amatuluka ndi kukalengeza kunja.

[7] Adani anga onse amanongʼonezana pamodzi kulimbana nane, iwo amalingalira zoyipa kwambiri za ine, ponena kuti,

[8] “Matenda owopsa amugwira; sadzaukapo pamalo pamene wagona.”

[9] Ngakhale bwenzi langa la pamtima amene ndinamudalira, iye amene amadya pamodzi ndi ine watukula chidendene chake kulimbana nane.

[10] Koma Yehova mundichititre chifundo, dzutseni kuti ndiwabwezere.

[11] Ine ndikudziwa kuti mukukondwera nane, pakuti mdani wanga sandigonjetsa.

[12] Mu ungwiro wanga Inu mumandisunga ndi kundiyimika pamaso panu kwamuyaya.

[13] Atamandike Yehova Mulungu wa Israeli kuchokera muyaya mpaka muyaya. q4 Ameni ndi Ameni.

Masalimo — Chapters