[1] Inu Yehova, musandidzudzule mu mkwiyo wanu, kapena kundilanga mu ukali wanu.
[2] Ndichitireni chifundo Inu Yehova, pakuti ndalefuka; Inu Yehova chiritseni, pakuti mafupa anga ali pa ululu waukulu.
[3] Moyo wanga uli pa mazunzo aakulu. Mpaka liti, Inu Yehova, mpaka liti?
[4] Tembenukani Inu Yehova, ndipo mundilanditse; pulumutseni chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika.
[5] Palibe amene amakukumbukirani pamene wamwalira; Amakutamandani ndani ali ku manda?
[6] Ine ndatopa ndi kubuwula; usiku wonse pa bedi panga pamadzaza ndi misozi yanga; ndimanyowetsa pogona panga ndi misozi.
[7] Maso anga atupa chifukwa cha chisoni; akulephera kuona chifukwa cha adani anga.
[8] Chokani kwa ine inu nonse amene mumachita zoyipa, pakuti Yehova wamva kulira kwanga.
[9] Yehova wamva kupempha kwanga kofuna chifundo; Yehova walandira pemphero langa.
[10] Adani anga onse adzachita manyazi ndipo adzakhala ndi mantha; adzabwerera msangamsanga mwa manyazi.