Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 6:44

[1] Tamandani Yehova. Yamikani Yehova chifukwa ndi wabwino; pakuti chikondi chake ndi chosatha.

[2] Ndani angathe kufotokoza za ntchito zamphamvu za Yehova kapena kumutamanda mokwanira?

[3] Odala ndi amene amasunga chilungamo, amene amachita zolungama nthawi zonse.

[4] Mundikumbukire Yehova, pamene mukuonetsa kukoma mtima kwanu kwa anthu anu, bwerani mudzandithandize pamene mukuwapulumutsa iwo,

[5] kuti ndidzasangalale ndi chuma cha anthu anu osankhika, kuti ndidzakhale nacho chimwemwe cha anthu anu ndi kukhala pamodzi ndi cholowa chanu pa kukutamandani.

[6] Ife tachimwa monga momwe anachitira makolo athu; tachita zolakwa ndipo tachita moyipa.

[7] Pamene makolo athu anali mu Igupto, sanalingalire za zozizwitsa zanu; iwo sanakumbukire kukoma mtima kwanu kochuluka, ndipo anawukira Inu pa Nyanja Yofiira.

[8] Komabe Iye anawapulumutsa chifukwa cha dzina lake, kuti aonetse mphamvu zake zazikulu.

[9] Anadzudzula Nyanja Yofiira, ndipo inawuma; anawatsogolera mʼnyanja yakuya ngati akuyenda mʼchipululu.

[10] Anawapulumutsa mʼdzanja la amaliwongo; anawawombola mʼdzanja la mdani.

[11] Madzi anamiza adani awo, palibe mmodzi wa iwo anapulumuka.

[12] Kenaka iwo anakhulupirira malonjezo ake ndi kuyimba nyimbo zamatamando.

[13] Koma posachedwa anayiwala zimene Iye anachita, ndipo sanayembekezere uphungu wake.

[14] Mʼchipululu, anadzipereka ku zilakolako zawo; mʼdziko lopanda kanthu anayesa Mulungu.

[15] Choncho Iye anawapatsa chimene anapempha, koma anatumiza nthenda yowondetsa.

[16] Mʼmisasa, anachitira nsanje Mose ndi Aaroni, amene Yehova anadzipatulira.

[17] Nthaka inatsekuka ndipo inameza Datani; inakwirira gulu la Abiramu.

[18] Moto unayaka pakati pa otsatira awo; lawi lamoto linapsereza anthu oyipa.

[19] Iwo anapanga mwana wangʼombe pa Horebu ndi kulambira fano loyengedwa kuchokera ku chitsulo.

[20] Anasinthanitsa ulemerero wawo ndi fano la ngʼombe yayimuna imene imadya udzu.

[21] Anayiwala Mulungu amene anawapulumutsa, amene anachita zinthu zazikulu mu Igupto,

[22] zozizwitsa mʼdziko la Hamu ndi machitidwe ake woopsa pa Nyanja Yofiira.

[23] Choncho Iye anawawuza kuti adzawawononga, pakanapanda Mose, mtumiki wake wosankhidwa, kuyima pamaso pake, ndi kuletsa mkwiyo wake kuti usawawononge.

[24] Motero iwo ananyoza dziko lokoma; sanakhulupirire malonjezo ake.

[25] Anangʼungʼudza mʼmatenti mwawo ndipo sanamvere Yehova.

[26] Kotero Iye analumbira atakweza dzanja lake, kuti adzachititsa kuti iwowo afere mʼchipululu,

[27] kuchititsa kuti zidzukulu zawo zifere pakati pa anthu a mitundu ina ndi kuwabalalitsa mʼdziko lonse.

[28] Iwo anayamba kupembedza Baala-Peori ndi kudya nsembe zoperekedwa kwa milungu yopanda moyo;

[29] anaputa mkwiyo wa Yehova pa machitidwe awo oyipa, ndipo mliri unabuka pakati pawo.

[30] Koma Finehasi anayimirira ndi kulowererapo, ndipo mliri unaleka.

[31] Chimenechi ndicho chinayesedwa chilungamo chake, kwa mibado yosatha imene ikubwera.

[32] Pa madzi a ku Meriba iwo anakwiyitsa Yehova ndipo mavuto anabwera kwa Mose chifukwa cha anthuwo,

[33] pakuti iwowo anawukira mzimu wa Mulungu, ndipo pa milomo ya Mose panatuluka mawu osayenera.

[34] Aisraeliwo sanawononge mitundu ya anthu monga momwe Yehova anawalamulira.

[35] Koma anasakanizana ndi anthu a mitundu inayo ndi kuphunzira miyambo yawo.

[36] Ndipo anapembedza mafano awo, amene anakhala msampha kwa iwowo.

[37] Anapereka nsembe ana awo aamuna ndi ana awo aakazi kwa ziwanda.

[38] Anakhetsa magazi a anthu osalakwa, magazi a ana awo aamuna ndi a ana awo aakazi, amene anawapereka nsembe kwa mafano a ku Kanaani, ndipo dziko linayipitsidwa ndi magazi awo.

[39] Iwo anadzidetsa okha ndi zimene anachita; ndi machitidwe awo amakhala ngati munthu wachigololo.

[40] Tsono Yehova anakwiya ndi anthu ake ndipo ananyansidwa ndi cholowa chake.

[41] Iye anawapereka kwa anthu a mitundu ina, ndipo adani awo anawalamulira.

[42] Adani awo anawazunza ndi kuwakhazika pansi pa mphamvu yawo.

[43] Iye ankawapulumutsa nthawi zambiri, koma iwo ankatsimikiza za kuwukira ndipo anawonongeka mʼmachimo awo.

[44] Koma Iye anaona kuzunzika kwawo pamene anamva kulira kwawo;

[45] Chifukwa cha iwo Iye anakumbukira pangano lake ndipo anawalezera mtima chifukwa cha kukula kwa chikondi chake.

[46] Iye anachititsa kuti amene anawagwira iwo ukapolo awamvere chisoni.

[47] Tipulumutseni Inu Yehova Mulungu wathu, ndipo mutisonkhanitse kuchoka kwa anthu a mitundu ina kuti tithe kuyamika dzina lanu loyera ndi kunyadira mʼmatamando anu.

[48] Atamandike Yehova, Mulungu wa Israeli, Kuyambira muyaya mpaka muyaya. Anthu onse anene kuti, “Ameni!” Tamandani Yehova.

Masalimo — Chapters