[1] Wamkulu ndi Yehova, ndi woyenera kwambiri matamando mu mzinda wa Mulungu wathu, phiri lake loyera.
[2] Lokongola mu utali mwake, chimwemwe cha dziko lonse lapansi. Malo aatali kwambiri a Zafoni ndiye Phiri la Ziyoni, mzinda wa Mfumu yayikulu.
[3] Mulungu ali mu malinga ake; Iye wadzionetsa yekha kuti ndiye malinga akewo.
[4] Pamene mafumu anasonkhana pamodzi, pamene anayendera pamodzi kudzalimbana nafe,
[5] iwo anaona mzindawo ndipo anadabwa kwambiri; anathawa ndi mantha aakulu.
[6] Pomwepo anagwidwa nako kunjenjemera, ululu wonga wa mkazi woyembekezera pa nthawi yochira.
[7] Inu munawawononga monga sitima zapamadzi za ku Tarisisi zitawonongeka ndi mphepo ya kummawa.
[8] Monga momwe tinamvera, kotero ife tinaona mu mzinda wa Yehova Wamphamvuzonse, mu mzinda wa Mulungu wathu. Mulungu adzawuteteza kwamuyaya.
[9] Mʼkati mwa Nyumba yanu Mulungu, ife timalingaliramo zachikondi chanu chosasinthika.
[10] Monga dzina lanu, Inu Mulungu, matamando anu amafika ku malekezero a dziko lapansi dzanja lanu lamanja ladzaza ndi chilungamo.
[11] Phiri la Ziyoni likukondwera, midzi ya Yuda ndi yosangalala chifukwa cha maweruzo anu.
[12] Yendayendani mu Ziyoni, uzungulireni mzindawo, werengani nsanja zake.
[13] Yangʼanitsitsani bwino mipanda yake, penyetsetsani malinga ake, kuti mudzafotokoze za izo ku mʼbado wotsatira.
[14] Pakuti Mulungu uyu ndi Mulungu wathu ku nthawi zosatha; Iye adzakhala mtsogoleri wathu mpaka ku mapeto.