Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 5:39

[1] Pulumutseni Inu Mulungu, pakuti madzi afika mʼkhosi

[2] Ine ndikumira mʼthope lozama mʼmene mulibe popondapo. Ndalowa mʼmadzi ozama; mafunde andimiza.

[3] Ndafowoka ndikupempha chithandizo; kummero kwanga kwawuma gwaa, mʼmaso mwanga mwada kuyembekezera Mulungu wanga.

[4] Iwo amene amadana nane popanda chifukwa ndi ochuluka kuposa tsitsi la kumutu kwanga; ambiri ndi adani anga popanda chifukwa, iwo amene akufunafuna kundiwononga. Ndikukakamizidwa kubwezera zomwe sindinabe.

[5] Mukudziwa uchitsiru wanga, Inu Mulungu, kulakwa kwanga sikuli kobisika kwa Inu.

[6] Iwo amene amadalira Inu asanyozedwe chifukwa cha ine, Inu Ambuye Wamphamvuzonse. Iwo amene amafunafuna Inu asachititsidwe manyazi chifukwa cha ine, Inu Mulungu wa Israeli.

[7] Pakuti ndimapirira kunyozedwa chifukwa cha Inu, ndipo manyazi amaphimba nkhope yanga.

[8] Ndine mlendo kwa abale anga, munthu wakudza kwa ana aamuna a amayi anga;

[9] pakuti changu chochitira nyumba yanu chandiphetsa ndipo chipongwe cha iwo amene amanyoza Inu chandigwera.

[10] Pamene ndikulira ndi kusala kudya, ndiyenera kupirira kunyozedwa;

[11] pomwe ndavala chiguduli, anthu amandiseweretsa.

[12] Iwo amene amakhala pa chipata amandinena, ndipo ine ndine nyimbo ya zidakwa.

[13] Koma ndikupempha kwa Inu Ambuye, pa nthawi yanu yondikomera mtima; mwa chikondi chanu chachikulu Inu Mulungu, mundiyankhe pondipulumutsa.

[14] Mundilanditse kuchoka mʼmatope, musalole kuti ndimire, pulumutseni ine kwa iwo amene amadana nane, kuchoka mʼmadzi ozama.

[15] Musalole kuti chigumula chindimeze, kuya kusandimeze ndipo dzenje lisatseke pakamwa pake kundimiza.

[16] Ndiyankheni Inu Yehova mwa ubwino wanu wa chikondi chanu; mwa chifundo chanu chachikulu tembenukirani kwa ine.

[17] Musabisire nkhope yanu mtumiki wanu, ndiyankheni msanga, pakuti ndili pa mavuto.

[18] Bwerani pafupi ndi kundilanditsa; ndiwomboleni chifukwa cha adani anga.

[19] Inu mukudziwa momwe ndanyozedwera, kunyozedwa ndi kuchititsidwa manyazi; adani anga onse ali pamaso panu.

[20] Mnyozo waswa mtima wanga ndipo wandisiya wopanda thandizo lililonse; ndinafunafuna ena woti andichitire chisoni, koma panalibe ndi mmodzi yemwe woti anditonthoze, sindinapeze ndi mmodzi yemwe.

[21] Iwo anayika ndulu mʼchakudya changa ndi kundipatsa vinyo wosasa chifukwa cha ludzu.

[22] Chakudya chomwe chayikidwa patsogolo pawo chikhale msampha; chikhale chobwezera chilango ndiponso khwekhwe.

[23] Maso awo adetsedwe kotero kuti asaonenso ndipo misana yawo ipindike mpaka kalekale.

[24] Khuthulirani ukali wanu pa iwo; mkwiyo wanu woyaka moto uwathe mphamvu.

[25] Malo awo akhale wopanda anthu pasapezeke ndi mmodzi yemwe wokhala mʼmatenti awo.

[26] Pakuti iwo amazunza amene inu munamuvulaza ndi kuyankhula zowawa kwa amene munawapweteka.

[27] Awonjezereni kulakwa pa kulakwa kwawo, musalole kuti akhale ndi gawo pa chipulumutso chanu.

[28] Iwo afufutidwe mʼbuku la amoyo ndipo asalembedwe pamodzi ndi olungama.

[29] Ndikumva zowawa ndi kuzunzika; lolani chipulumutso chanu, Inu Mulungu, chinditeteze.

[30] Ine ndidzatamanda dzina la Mulungu mʼnyimbo, ndidzalemekeza Iye ndi chiyamiko.

[31] Izi zidzakondweretsa Yehova kupambana ngʼombe, kupambananso ngʼombe yayimuna, pamodzi ndi nyanga ndi ziboda zake.

[32] Wosauka adzaona ndipo adzasangalala, Inu amene mumafunafuna Mulungu, mitima yanu ikhale ndi moyo!

[33] Yehova amamvera anthu osowa ndipo sanyoza anthu ake omangidwa.

[34] Kumwamba ndi dziko lapansi zitamanda Iye, nyanja ndi zonse zomwe zimayenda mʼmenemo,

[35] pakuti Mulungu adzapulumutsa Ziyoni ndi kumanganso mizinda ya Yuda, anthu adzakhala kumeneko ndipo dzikolo lidzakhala lawo;

[36] ana atumiki ake adzalitenga kukhala cholowa chawo, ndipo iwo amene amakonda dzina lake adzakhala kumeneko.

Masalimo — Chapters