[1] Yehova imvani pemphero langa; kulira kwanga kopempha thandizo kufike kwa Inu.
[2] Musandibisire nkhope yanu pamene ndili pa msautso. Munditcherere khutu; pamene ndiyitana ndiyankheni msanga.
[3] Pakuti masiku anga akupita ngati utsi; mafupa anga akunyeka ngati nkhuni zoyaka.
[4] Mtima wanga wakanthidwa ndipo ukufota ngati udzu; ndipo ndimayiwala kudya chakudya changa.
[5] Chifukwa cha kubuwula kwanga kofuwula ndatsala chikopa ndi mafupa okhaokha.
[6] Ndili ngati kadzidzi wa ku chipululu, monga kadzidzi pakati pa mabwinja.
[7] Ndimagona osapeza tulo; ndakhala ngati mbalame yokhala yokha pa denga.
[8] Tsiku lonse adani anga amandichita chipongwe; iwo amene amandinyoza, amagwiritsa ntchito dzina langa ngati temberero.
[9] Pakuti ndimadya phulusa ngati chakudya changa ndi kusakaniza chakumwa changa ndi misozi
[10] chifukwa cha ukali wanu waukulu, popeza Inu mwandinyamula ndi kunditayira kumbali.
[11] Masiku anga ali ngati mthunzi wa kumadzulo; Ine ndikufota ngati udzu.
[12] Koma Inu Yehova, muli pa mpando wanu waufumu kwamuyaya; kudziwika kwanu ndi kokhazikika ku mibado yonse.
[13] Inu mudzadzuka ndi kuchitira chifundo Ziyoni pakuti ndi nthawi yoti muonetse kukoma mtima kwanu pa iyeyo; nthawi yoyikika yafika.
[14] Pakuti miyala yake ndi yokondedwa kwa atumiki anu; fumbi lake lokha limawachititsa kuti amve chisoni.
[15] Mitundu ya anthu idzaopa dzina la Yehova, mafumu onse a dziko lapansi adzalemekeza ulemerero wanu.
[16] Pakuti Yehova adzamanganso Ziyoni ndi kuonekera mu ulemerero wake.
[17] Iye adzayankha pemphero la anthu otayika; sadzanyoza kupempha kwawo.
[18] Zimenezi zilembedwe chifukwa cha mibado ya mʼtsogolo, kuti anthu amene sanabadwe adzatamande Yehova:
[19] “Yehova anayangʼana pansi kuchokera ku malo ake opatulika mmwamba, kuchokera kumwamba anayangʼana dziko lapansi,
[20] kuti amve kubuwula kwa anthu a mʼndende, kuti apulumutse amene anayenera kuphedwa.”
[21] Kotero dzina la Yehova lidzalengezedwa mu Ziyoni ndi matamando ake mu Yerusalemu,
[22] pamene mitundu ya anthu ndi maufumu adzasonkhana kuti alambire Yehova.
[23] Iye anathyola mphamvu zanga pa nthawi ya moyo wanga; Iyeyo anafupikitsa masiku anga.
[24] Choncho Ine ndinati: “Musandichotse, Inu Mulungu wanga, pakati pa masiku a moyo wanga; zaka zanu zimakhalabe pa mibado yonse.
[25] Pachiyambi Inu munakhazikitsa maziko a dziko lapansi ndipo mayiko akumwamba ndi ntchito ya manja anu.
[26] Izi zidzatha, koma Inu mudzakhalapo; zidzatha ngati chovala. Mudzazisintha ngati chovala ndipo zidzatayidwa.
[27] Koma Inu simusintha, ndipo zaka zanu sizidzatha.
[28] Ana a atumiki anu adzakhala pamaso panu; zidzukulu zawo zidzakhazikika pamaso panu.”