Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 3:41

[1] Pamenepo Bilidadi wa ku Suki anayankha kuti,

[2] “Kodi udzakhala ukuyankhula zoterezi mpaka liti? Mawu ako ali ngati mphepo yamkuntho.

[3] Kodi Mulungu amapotoza chiweruzo cholungama? Kodi Wamphamvuzonse amalephera kuchita zachilungamo?

[4] Pamene ana ako anamuchimwira Mulungu, Iye anawapereka kuti alangidwe chifukwa cha tchimo lawo.

[5] Koma utayangʼana kwa Mulungu, ndi kudandaulira Wamphamvuzonse,

[6] ngati uli wangwiro ndi wolungama mtima ngakhale tsopano Iye adzachitapo kanthu mʼmalo mwako ndipo adzakubwezeretsa pa malo ako oyenera.

[7] Chiyambi chako chidzaoneka ngati chochepa koma chimaliziro chako chidzakhala chopambana.

[8] “Funsa kwa anthu amvulazakale ndipo upeze zimene makolo awo anaziphunzira

[9] pakuti ife ndife ana adzulodzuloli ndipo sitidziwa chilichonse, ndipo moyo wathu pa dziko lapansi uli ngati chithunzithunzi.

[10] Kodi iwo sadzakulangiza ndi kukufotokozera? Kodi sadzakuwuza mawu ochokera pa zimene amazidziwa?

[11] Kodi bango nʼkumera pa nthaka yopanda chinyontho? Nanga mawango nʼkukula bwino popanda madzi?

[12] Popanda madzi, zimenezi zimafota zikanali zaziwisi ndi zosadula; zimawuma msangamsanga kuposa bango.

[13] Ndimo mmene amachitira anthu onse amene amayiwala Mulungu; ndi mmene chiyembekezo cha munthu wosapembedza Mulungu chimathera.

[14] Kulimba mtima kwake kumafowoka; zimene iye amadalira zili ngati ukonde wa kangawude.

[15] Iye amatsamira ukonde wake, koma umaduka; amawugwiritsitsa koma sulimba.

[16] Munthu woyipayo ali ngati chomera chothiriridwa bwino chimene chili pa dzuwa, nthambi zake zimatambalala pa munda wake;

[17] mizu yake imayanga pa mulu wa miyala ndi kufunafuna malo woti izikike pa miyalapo.

[18] Koma pamene yachotsedwa pamalo pakepo, pamalopo pamakana chomeracho ndi kuti, ‘Ine sindinakuonepo.’

[19] Ndithudi chomeracho chimafota, ndipo pa nthakapo pamatuluka zomera zina.

[20] “Ndithudi, Mulungu sakana munthu amene alibe cholakwa kapena kulimbikitsa anthu ochita zoyipa.

[21] Iye adzadzaza mʼkamwa mwako ndi phwete ndipo milomo yako idzafuwula ndi chimwemwe.

[22] Adani ako adzachita manyazi, ndipo malo okhalamo anthu oyipa sadzaonekanso.”

Yobu — Chapters