Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 3:42

[1] Tsono anthu atatuwa analeka kumuyankha Yobu, chifukwa chakuti iyeyo ankadziona kuti ndi wolungama.

[2] Koma Elihu, mwana wa Barakeli, wa fuko la Buzi, wa banja la Ramu, anapsera mtima kwambiri Yobu chifukwa choti Yobuyo anakana kuvomera kuti anachimwa ndi kuti Mulungu anakhoza pomulanga.

[3] Anapseranso mtima abwenzi ake atatu aja chifukwa sanapeze njira yomutsutsira Yobu, ngakhale iwo anamupeza kuti anali wolakwa.

[4] Tsono Elihu anadikira kuti ayankhule ndi Yobu chifukwa choti abwenziwo anali akuluakulu kupambana iyeyo.

[5] Koma Elihu ataona kuti anthu atatuwo analibe mawu oti ayankhulenso, iye anapsa mtima.

[6] Choncho Elihu mwana wa Barakeli wa fuko la Buzi anati: “Ine ndine wamngʼono, inuyo ndinu akuluakulu, nʼchifukwa chake ndimaopa, ndimachita mantha kuti ndikuwuzeni zimene ndimadziwa.

[7] Ndimaganiza kuti, ‘Ayambe ndi akuluakulu kuyankhula; anthu amvulazakale ndiwo amaphunzitsa nzeru.’

[8] Koma mzimu wa Mulungu mwa munthu, mpweya wa Wamphamvuzonse, ndi umene umapereka nzeru zomvetsa zinthu.

[9] Si okalamba amene ali ndi nzeru, si amvulazakale okha amene ali ndi nzeru zomvetsa zinthu zimene zili zoyenera.

[10] “Nʼchifukwa chake ndikuti, ‘Mvereni; inenso ndikukuwuzani zimene ndikuzidziwa.’

[11] Ndadikira nthawi yonseyi, ndimamvetsera mwachidwi zimene mumayankhula, pamene mumafunafuna mawu oti muyankhule,

[12] ineyo ndinakumvetseranidi. Koma palibe ndi mmodzi yemwe wa inu amene anatsutsa Yobu; palibe aliyense wa inu amene anamuyankha mawu ake.

[13] Musanene kuti, ‘Ife tapeza nzeru; Mulungu ndiye amutsutse, osati munthu.’

[14] Koma Yobu sanayankhule motsutsana ndi ine, ndipo ine sindimuyankha monga mmene inu mwamuyankhira.

[15] “Iwo asokonezeka ndipo alibe choti ayankhulenso; mawu awathera.

[16] Kodi ine ndidikire chifukwa iwo sakuyankhula tsopano, pakuti angoyima phee wopanda yankho?

[17] Inenso ndiyankhulapo tsopano; nanenso ndinena zimene ndikudziwa.

[18] Pakuti ndili nawo mawu ambiri, ndipo mtima wanga ukundikakamiza;

[19] mʼkati mwanga ndili ngati botolo lodzaza ndi vinyo, ngati matumba a vinyo watsopano amene ali pafupi kuphulika.

[20] Ndiyenera kuyankhula kuti mtima utsike; ndiyenera kutsekula pakamwa panga ndi kuyankha.

[21] Sindidzakondera munthu wina aliyense, kapena kuyankhula zoshashalika,

[22] pakuti ndikanakhala wa luso loyankhula moshashalika, Mlengi wanga akanandilanga msanga.”

Yobu — Chapters