Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 4:50

[1] “Koma tsopano, inu abambo Yobu chonde mverani mawu anga; mutcherere khutu zonse zimene ndinene.

[2] Tsopano ndiyamba kuyankhula; mawu anga ali pa msonga ya lilime langa.

[3] Mawu anga akuchokera mu mtima wolungama; pakamwa panga pakuyankhula zoonadi zimene ndikuzidziwa.

[4] Mzimu wa Mulungu wandiwumba, mpweya wa Wamphamvuzonse umandipatsa moyo.

[5] Mundiyankhe ngati mungathe; konzekani tsopano kuti munditsutse.

[6] Ine ndili monga inu pamaso pa Mulungu; nanenso ndinachokera ku dothi.

[7] Musachite mantha ndipo musandiope ayi, Ine sindikupanikizani kwambiri ayi.

[8] “Koma inu mwayankhula ine ndikumva, ndamva mawu anuwo onena kuti,

[9] ‘Ndine wolungama mtima ndi wopanda tchimo; ndine woyera mtima ndipo ndilibe cholakwa.

[10] Komatu Mulungu wapeza zifukwa zoti anditsutsire nazo; Iye akundiyesa ngati mdani wake.

[11] Iyeyo wamanga mapazi anga mʼzigologolo, akulonda mayendedwe anga onse.’

[12] “Koma ine ndi kuti kwa inu, inuyo simukukhoza pa zimenezi, pakuti Mulungu ndi wamkulu kupambana munthu.

[13] Chifukwa chiyani mukudandaula kwa Iye kuti sayankha mawu ena aliwonse a munthu?

[14] Pajatu Mulungu amayankhula mwa njira zosiyanasiyana, ngakhale munthu sazindikira zimenezi.

[15] Mʼmaloto, mʼmasomphenya usiku, pamene anthu ali mʼtulo tofa nato pamene akungosinza chabe pa bedi,

[16] amawanongʼoneza mʼmakutu ndi kuwaopseza ndi machenjezo ake,

[17] kumuchotsa munthu ku zoyipa, ndi kuthetseratu kunyada kwake,

[18] kumulanditsa munthu ku manda, kuti moyo wake usawonongeke ndi lupanga.

[19] “Mwina Mulungu amalanga munthu ndi matenda ndi ululu ali pa bedi pake, nthawiyo thupi lake lonse limangophwanya,

[20] kuti asakhalenso ndi chilakolako cha chakudya, ndipo amanyansidwa ndi chakudya chabwino chomwe.

[21] Thupi lake limawonda ndipo mafupa ake, omwe anali obisika, tsopano amaonekera poyera.

[22] Munthuyo amayandikira ku manda, moyo wake umayandikira kwa amene amabweretsa imfa.

[23] “Koma patakhala mngelo ngati mthandizi, mmodzi mwa ambirimbiri oterewa, adzafotokoza zimene zili zoyenera,

[24] kudzamukomera mtima ndi kunena kuti, ‘Mupulumutseni kuti asapite ku manda; ine ndapeza cholowa mʼmalo mwa moyo wake,’

[25] pamenepo thupi lake lidzasanduka lasee ngati la mwana; ndipo adzabwezeretsedwanso kukhala ngati mʼmasiku a unyamata wake.

[26] Akapemphera kwa Mulungu, iyeyo adzalandiridwa. Mulungu adzamulandira mwa chimwemwe ndipo adzamubwezeretsa pamalo ake oyamba.

[27] Ndipo adzabwera kwa anzake ndi kunena kuti, ‘Ndinachimwa ndipo sindinachite zolungama, koma sindinalangidwe koyenerana ndi kuchimwa kwanga.

[28] Iye anapulumutsa moyo wanga kuti usapite ku manda, ndipo ndidzakhala ndi moyo ndi kuonanso kuwala kwa dzuwa.’

[29] “Mulungu amachita zonsezi kwa munthu kawirikawiri,

[30] kupulumutsa moyo wa munthuyo ku manda, kuti athe kuonanso kuwala kwa moyo.

[31] “Abambo Yobu, tcherani khutu ndipo mundimvere; khalani chete kuti ndiyankhule.

[32] Ngati muli nʼchoti munene, ndiyankheni; yankhulani, pakuti ine ndikufuna mupezeke wolungama.

[33] Koma ngati sichoncho, mundimvere; khalani chete ndipo ine ndidzakuphunzitsani nzeru.”

Yobu — Chapters