[1] Pamenepo Yobu anayankha kuti,
[2] “Kodi mudzakhala mukundizunza mpaka liti, ndi kundilasa ndi mawu anuwo?
[3] Inuyo mwandinyoza kwambiri; mwanditsutsa mopanda manyazi.
[4] Ngati ndi zoona kuti ine ndasochera, cholakwachotu nʼchanga.
[5] Ngati ndithudi mukudziyika nokha pamwamba panga, ndi kugwiritsa ntchito kunyozedwa kwanga polimbana nane,
[6] pamenepa dziwani kuti Mulungu wandilakwira ndipo wandizinga ukonde wake.
[7] “Ngakhale ndifuwule kuti, ‘Akundizunza!’ Palibe wondiyankha; ngakhale ndipemphe thandizo, palibe wondichitira zolungama.
[8] Mulungu wanditsekera njira yanga kotero sindingathe kudutsa; waphimba njira zanga ndi mdima.
[9] Iye wandilanda ulemu wanga ndipo wandivula chipewa chaufumu pamutu panga.
[10] Wandiphwanyaphwanya mbali zonse ndipo ndatheratu; Iye wazula chiyembekezo changa ngati mtengo.
[11] Wandikwiyira ndipo akundiyesa mmodzi mwa adani ake.
[12] Ankhondo ake akubwera kwa ine mwamphamvu, akonzekera zodzalimbana nane ndipo azungulira nyumba yanga.
[13] “Mulungu wandisiyanitsa ndi abale anga; wasandutsa odziwana nane kukhala achilendo kwa ine.
[14] Abale anga andithawa; abwenzi anga andiyiwala.
[15] Anthu odzacheza ku nyumba kwanga ndiponso antchito anga aakazi andisandutsa mlendo; ndasanduka mlendo mʼmaso mwawo.
[16] Ndikayitana wa ntchito wanga, iye sandiyankha, ngakhale ndikapempha ndi pakamwa panga sandichitira kanthu.
[17] Mpweya wanga umamunyansa mkazi wanga; ndine chinthu chonyansa kwa abale anga a mimba imodzi.
[18] Inde, ngakhale ana amandinyoza; akandiona amandinyodola.
[19] Anzanga onse apamtima amanyansidwa nane; iwo amene ndinkawakonda andiwukira.
[20] Ndangotsala khungu ndi mafupa okhaokha; ndapulumuka lokumbakumba.
[21] “Mvereni chisoni, inu abwenzi anga, mvereni chisoni, pakuti dzanja la Mulungu landikantha.
[22] Chifukwa chiyani mukundilondola ngati Mulungu? Kodi simunatope nalo thupi langa?
[23] “Aa, achikhala mawu anga analembedwa, achikhala analembedwa mʼbuku,
[24] akanalembedwa pa mwala ndi chitsulo, akanalembedwa pa thanthwe kuti sangathe kufufutidwa!
[25] Koma ndikudziwa kuti mpulumutsi wanga ali ndi moyo, ndipo pa nthawi yomaliza adzabwera kudzanditeteza.
[26] Ndipo khungu langa litatha nʼkuwonongeka, mʼthupi langa lomweli ndidzamuona Mulungu.
[27] Ine ndemwe ndidzamuona Iye ndi maso angawa, ineyo, osati wina ayi. Ndithu mtima wanga ukufunitsitsadi!
[28] “Koma inu mukuti, ‘Haa! Tingamuzunze bwanji, popeza kuti zonsezi zaoneka chifukwa cha iye yemweyo?’
[29] Inu muyenera kuopa lupanga; pakuti mkwiyo wake umalangadi ndi lupanga; zikadzatero muzadziwa kuti chiweruzo chilipo ndithu.”