Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 2:21

[1] Ndipo Elihu anawonjeza kunena kuti,

[2] “Kodi mukuganiza kuti mukukhoza? Mukunena kuti, ‘Ndine wolungama pamaso pa Mulungu.’

[3] Komanso inu mukufunsa kuti, ‘Kodi phindu langa nʼchiyani, ndipo ndimapeza chiyani ndikapanda kuchimwa?’

[4] “Ine ndikufuna ndikuyankheni inu pamodzi ndi abwenzi anu omwe.

[5] Yangʼanani kumwamba ndipo muone mitambo imene ili kutali ndi inuyo.

[6] Inuyo mukachimwa, Iye zimamukhudza motani? Ngati machimo anu ndi ochuluka, zimenezo zimachita chiyani kwa Iye?

[7] Ngati inu ndinu wolungama, mumamupatsa Iyeyo chiyani? Kapena Iye amalandira chiyani chochokera mʼdzanja lanu?

[8] Kuyipa kwanu kumangokhudza anthu ngati inuyo, ndipo chilungamo chanu chimakhudza anthu anzanu.

[9] “Anthu akufuwula chifukwa cha kuzunzidwa; akufuna chithandizo kuti achoke pansi pa ulamuliro wa anthu amphamvu.

[10] Koma palibe amene akunena kuti, ‘Kodi ali kuti Mulungu, Mlengi wanga, amene amatisangalatsa nthawi ya usiku,

[11] amene amatiphunzitsa kupambana nyama za dziko lapansi ndipo amatipatsa nzeru kupambana mbalame zowuluka?’

[12] Iye sayankha pamene anthu akufuwulira kwa Iye chifukwa cha kudzikuza kwa anthu oyipa.

[13] Ndithu, Mulungu samva kupempha kwawo kopanda pake; Wamphamvuzonse sasamalira zimenezi.

[14] Ndipo ndi bodza lalikulu kunena kuti Iye saona zimene zikuchitika. Iye adzaweruza molungama ngati inu mutamudikira

[15] ndiye tsono popeza kuti ukali wake sukupereka chilango, zoyipa zambiri zimene anthu amachita,

[16] abambo Yobu mumangoyankhula zopandapake, mukungochulukitsa mawu opanda nzeru.”

Yobu — Chapters