[1] Pamenepo Yobu anayankha kuti,
[2] “Wamuthandizadi munthu wopanda mphamvu! Walimbitsadi dzanja la munthu wofowoka!
[3] Wapereka malangizo kwa munthu amene alibe nzeru! Ndipotu waonetsadi nzeru zochuluka!
[4] Kodi wakuthandiza ndani kuti uyankhule mawu awa? Ndipo ndi mzimu wa yani umene unayankhula pakamwa pako?
[5] “Mizimu ya anthu akufa ikunjenjemera pansi pa madzi, ndi zonse zokhala mʼmadzimo.
[6] Dziko la anthu akufa ndi lapululu pamaso pa Mulungu; chiwonongeko ndi chosaphimbidwa.
[7] Mulungu anayala thambo la kumpoto pa phompho; Iye anakoloweka dziko lapansi mʼmalo mwake pamene panali popanda nʼkanthu komwe.
[8] Amasunga madzi ambiri mʼmitambo yake, koma mitamboyo siphulika chifukwa cha kulemera kwa madziwo.
[9] Iye amaphimba mwezi wowala, amawuphimba ndi mitambo yake.
[10] Mulungu anawalembera madzi malire wonga uta, kukhala malire pakati pa kuwunika ndi mdima.
[11] Mizati yochirikiza mitambo yakumwamba imanjenjemera, ndi kudabwa pa kudzudzula kwake.
[12] Ndi mphamvu zake anatontholetsa nyanja; ndi nzeru zake anakantha chirombo cha mʼmadzi chija chotchedwa Rahabe.
[13] Ndi mpweya wake anayeretsa zamumlengalenga, dzanja lake linapha chinjoka chothawa chija.
[14] Zimenezi ndi pangʼono chabe mwa ntchito yake; tingomva pangʼono za Iye ngati kunongʼona! Kodi ndani angathe kudziwa kukula kwa mphamvu zake?”