Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 3:15

[1] Pamenepo Bilidadi wa ku Suki anayankha kuti,

[2] “Kodi iwe Yobu utsiriza liti zoyankhula zakozi? Khala munthu wozindikira zinthu ndipo ukatero ife tidzayankhula.

[3] Chifukwa chiyani ukutiyesa ngati ngʼombe ndi kuoneka ngati opusa mʼmaso mwako?

[4] Iwe amene ukudzipweteka wekha ndi mkwiyo wako, kodi dziko lapansi lisanduke bwinja chifukwa cha iweyo? Kodi kapena thanthwe lisunthidwe kuchoka pa malo ake?

[5] “Nyale ya munthu woyipa yazimitsidwa; malawi a moto wake sakuwalanso.

[6] Kuwala kwa mʼnyumba mwake kwasanduka mdima; nyale ya pambali pake yazima.

[7] Mayendedwe ake amgugu azilala; fundo zake zomwe zamugwetsa.

[8] Mapazi ake amulowetsa mu ukonde ndipo akungoyendayenda mu ukondewo.

[9] Msampha wamkola mwendo; khwekhwe lamugwiritsitsa.

[10] Amutchera msampha pansi mobisika; atchera diwa pa njira yake.

[11] Zoopsa zikumuchititsa mantha kumbali zonse, zikutsatira mayendedwe ake onse.

[12] Mphamvu zake zatha chifukwa cha njala, tsoka likumudikira.

[13] Wagwidwa nthenda yoopsa thupi lonse; miyendo yake, manja ake, zonse zawola.

[14] Wachotsedwa mʼnyumba imene ankadalira, ndipo amukokera ku imfa, mfumu ya zoopsa zonse.

[15] Mʼnyumba mwake zonse zachotsedwamo; awazamo sulufule kuti aphe tizirombo ta matenda.

[16] Mizu yake ikuwuma pansi ndipo nthambi zake zikufota

[17] Sadzakumbukiridwanso pa dziko lapansi; sadzakhalanso ndi chinthu chomutchukitsa mʼdziko.

[18] Amuchotsa pa malo owala ndi kumuponya ku mdima, ndipo amupirikitsa pa dziko lonse.

[19] Iye alibe ana kapena zidzukulu pakati pa anthu ake, kulibe wotsala kumene iye ankakhala.

[20] Anthu akumadzulo adabwa kwambiri ndi tsoka lake; anthu akummawa agwidwa ndi mantha aakulu.

[21] Ndithudi, izi ndiye zimagwera munthu woyipa; amenewa ndiye mathero a munthu amene sadziwa Mulungu.”

Yobu — Chapters