Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 3:50

[1] Yobu anapitiriza kuyankhula kwake:

[2] “Aa! Ndikanakhala momwe ndinalili miyezi yapitayi, masiku amene Mulungu ankandiyangʼanira,

[3] pamene nyale yake inkandiwunikira ndipo ndi kuwunika kwakeko ine ndinkatha kuyenda mu mdima!

[4] Ndithu, masiku amene ndinali pabwino kwambiri, pamene ubwenzi wa Mulungu unkabweretsa madalitso pa nyumba yanga,

[5] nthawi imene Wamphamvuzonse anali nane, ndipo ana anga anali atandizungulira mʼmbalimu,

[6] pamene popondapo ine panali patakhathamira mafuta a mkaka, ndipo pa thanthwe pamatuluka mitsinje ya mafuta a olivi.

[7] “Pamene ndinkapita pa chipata cha mzinda ndi kukhala pa mpando wanga pabwalo,

[8] anyamata amati akandiona ankapatuka ndipo anthu akuluakulu ankayimirira;

[9] atsogoleri ankakhala chete ndipo ankagwira pakamwa pawo;

[10] anthu otchuka ankangoti duu, ndipo malilime awo anali atamatirira ku nkhama zawo.

[11] Aliyense amene anamva za ine anayankhula zabwino zanga, ndipo iwo amene anandiona ankandiyamikira,

[12] chifukwa ndinkapulumutsa mʼmphawi wofuna chithandizo, ndiponso mwana wamasiye amene analibe aliyense womuthandiza.

[13] Munthu amene anali pafupi kufa ankandidalitsa; ndinkasangalatsanso mkazi wamasiye.

[14] Chilungamo chinali ngati chovala changa; chiweruzo cholungama ndiye chinali mkanjo ndi nduwira yanga.

[15] Ndinali ngati maso kwa anthu osapenya; ndinali ngati mapazi kwa anthu olumala.

[16] Ndinali ngati abambo kwa anthu aumphawi; ndinkayimira mlendo pa mlandu wake.

[17] Ndinkawononga mphamvu za anthu oyipa ndi kulanditsa amene anali atagwidwa.

[18] “Ndinkaganiza kuti, ‘Ndidzafera mʼnyumba yanga, masiku a moyo wanga ali ochuluka ngati mchenga.

[19] Mizu yanga idzatambalalira ku madzi, ndipo mame adzakhala pa nthambi zanga usiku wonse.

[20] Ulemerero wanga udzakhala wosaguga mwa ine, ndipo uta wanga udzakhala watsopano nthawi zonse mʼdzanja langa.’

[21] “Anthu ankamvetsera zimene ndinkanena mwachidwi, ankadikira atakhala chete kuti amve malangizo anga.

[22] Ndikayankhula, iwo sankayankhulanso; mawu anga ankawagwira mtima.

[23] Ankayembekezera ine monga momwe amayembekezera mvula ndipo ankalandira mawu anga ngati mvula ya mʼmalimwe.

[24] Ndikawasekerera, iwo sankatha kukhulupirira; kuwala kwa nkhope yanga chinali chinthu chamtengowapatali kwa iwowo.

[25] Ndinkawasankhira njira yawo ndipo ndinkawatsogolera ngati mfumu; ndinkakhala ngati mfumu pakati pa gulu lake lankhondo; ndinali ngati msangalatsi pakati pa anthu olira.”

Yobu — Chapters