[1] “Ndaziona ndi maso anga zonsezi, ndazimva ndi makutu anga ndipo ndazimvetsa.
[2] Zimene inu mukudziwa, inenso ndimazidziwa; ineyo sindine munthu wamba kwa inu.
[3] Koma ine ndikulakalaka nditayankhula ndi Wamphamvuzonse ndi kukamba mlandu wanga ndi Mulungu.
[4] Koma inu mukundipaka mabodza; nonsenu ndinu asingʼanga opanda phindu!
[5] Achikhala munangokhala chete nonsenu! Apo mukanachita zanzeru.
[6] Tsopano imvani kudzikanira kwanga; imvani kudandaula kwa pakamwa panga.
[7] Kodi inu mudzayankhula moyipa kuyankhulira Mulungu? Kodi mudzayankhulira Iyeyo mwachinyengo?
[8] Kodi mudzaonetsa kuti Iyeyo ngokondera? Kodi inu mudzamuteteza Mulungu pa mlandu wake?
[9] Mulungu atayangʼanitsitsa, inu nʼkukupezani wosalakwa? Kodi inu mungamunamize Iye monga momwe munganamizire munthu?
[10] Ndithudi, Iye angathe kukudzudzulani ngati muchita zokondera mseri.
[11] Kodi ulemerero wake sungakuopseni? Kodi kuopsa kwake sikungakuchititseni mantha?
[12] Mawu anu anzeru ali ngati miyambi yopanda tanthauzo; mawu anu odzitchinjirizira ali ngati mpanda wadothi.
[13] “Khalani chete ndipo ndilekeni ndiyankhule; tsono zimene zindichitikire zichitike.
[14] Chifukwa chiyani ndikuyika moyo wanga pa chiswe ndi kutengera mʼmanja moyo wangawu?
[15] Ngakhale Iye andiphe, komabe ndidzamukhulupirira; ndithu, ndidzafotokoza mlandu wanga pamaso pake.
[16] Zoonadi, ichi ndiye chidzakhala chipulumutso changa pakuti palibe munthu wosapembedza amene angafike pamaso pake!
[17] Mvetserani mosamala mawu anga; makutu anu amve zimene ndikunena.
[18] Pakuti tsopano ndawukonzekera mlandu wanga, ndikudziwa ndipo adzandipeza wolungama.
[19] Kodi alipo wina amene angatsutsane nane? ngati zili choncho, ndidzakhala chete ndi kufa.
[20] “Inu Mulungu, ndipatseni zinthu ziwiri izi, ndipo pamenepo ine sindidzakubisalirani:
[21] Muchotse dzanja lanu pa ine, ndipo muleke kundichititsa mantha ndi kuopsa kwanuko.
[22] Tsono muyitane ndipo ndidzayankha, kapena mulole kuti ine ndiyankhule ndipo Inu muyankhe.
[23] Kodi zolakwa zanga ndi zingati ndipo machimo anga ndi angati? Wonetseni kulakwa kwanga ndi machimo anga.
[24] Chifukwa chiyani mukundifulatira ndi kundiyesa ine mdani wanu?
[25] Kodi mudzazunza tsamba lowuluka ndi mphepo? Kodi mudzathamangitsa mungu wowuma?
[26] Pakuti Inu mwalemba zinthu zowawa zonditsutsa nazo ndipo mukundipaka machimo a pa ubwana wanga.
[27] Inu mwamanga miyendo yanga ndi maunyolo. Mumayangʼanitsitsa mayendedwe anga onse poyika zizindikiro pamene mapazi anga apondapo.
[28] “Motero munthu amatha ngati chinthu chofumbwa, ngati chovala chodyedwa ndi njenjete.