[1] Ndipo Elihu anapitirira kuyankhula nati:
[2] “Mundilole pangʼono pokha ndipo ndikuonetsani kuti zilipo zambiri zoti ziyankhulidwe mʼmalo mwa Mulungu.
[3] Nzeru zanga ndimazitenga kutali; ndidzaonetsa kulungama kwa Mlengi wanga.
[4] Ndithudi mawu anga si abodza; wanzeru zangwiro ali ndi inu.
[5] “Mulungu ndi wamphamvu, koma sanyoza anthu; Iye ndi wamphamvu, ndipo ndi wokhazikika pa cholinga chake.
[6] Salola oyipa kuti akhalebe ndi moyo koma amapereka ufulu kwa anthu osautsidwa.
[7] Iye saleka kuyangʼanira anthu olungama; amawayika kuti alamulire pamodzi ndi mafumu ndipo amawalemekeza mpaka muyaya.
[8] Koma ngati anthu amangidwa ndi unyolo, ndipo akondwa ndi zingwe zamasautso,
[9] Iye amawafotokozera zomwe anachita, kuti iwo anachimwa modzikuza.
[10] Mulungu amawatsekula makutu kuti amve malangizo ake ndipo amawalamula kuti alape zoyipa zawo.
[11] Ngati iwo amumvera ndi kumutumikira, adzatsiriza masiku a moyo wawo mwamtendere, adzatsiriza zaka zawo mosangalala.
[12] Koma ngati samvera, adzaphedwa ndi lupanga ndipo adzafa osadziwa kanthu.
[13] “Anthu osapembedza amasunga mkwiyo mu mtima mwawo; akawalanga, safuwulira kwa Iye kupempha thandizo.
[14] Amafa akanali achinyamata, pakati pa amuna achiwerewere a kumalo azipembedzo.
[15] Koma ovutika, Iye amawapulumutsa pa mavuto awo; Mulungu amawayankhula mʼmasautso awowo.
[16] “Iye akukukopani inu kuti muchoke mʼmasautso, kuti mupite ku malo aakulu kumene kulibe chokutchingani, kumalo a mpumulo kumene kuli chakudya chabwino kwambiri.
[17] Koma tsopano inu mwapezeka wopalamula chifukwa cha kuyipa kwanu; chiweruzo ndi chilungamo chakugwerani.
[18] Muchenjere kuti wina asakukopeni ndi chuma; musalole kuti chiphuphu chachikulu chikusocheretseni.
[19] Kodi chuma chanu kapena mphamvu zanu zonse zingakusungeni kotero kuti simungakhale pa masautso?
[20] Musalakalake kuti usiku ubwere, pakuti ndiyo nthawi imene anthu adzawonongeka.
[21] Muchenjere kuti musatembenukire ku uchimo, chifukwa uchimowo ndiwo unabweretsa kuzunzika kwanu.
[22] “Taonani, Mulungu ndi wamkulu ndiponso ndi wamphamvu. Kodi ndi mphunzitsi uti amene angafanane naye?
[23] Kodi ndani amene anamuwuzapo Mulungu zoti achite, kapena kumuwuza kuti, ‘Inu mwachita chinthu cholakwa?’
[24] Kumbukirani kutamanda ntchito zake zimene anthu amaziyamika mʼnyimbo.
[25] Anthu onse amaziona ntchitozo; anthuwo amaziona ali kutali.
[26] Ndithudi, Mulungu ndi wamkulu, sitimudziwa nʼpangʼono pomwe! Chiwerengero cha zaka zake nʼchosadziwika.
[27] “Mulungu ndiye amakweza timadontho tamadzi kuthambo, timene timasungunuka nʼkukhala mvula;
[28] mitambo imagwetsa mvulayo ndipo mvulayo imavumbwa pa anthu mokwanira.
[29] Kodi ndani amene angadziwe momwe mitambo imayendera, momwe Iye amabangulira kuchokera kumalo ake?
[30] Taonani momwe amawalitsira zingʼaningʼani pa malo ake onse, zimafika ngakhale pansi pa nyanja.
[31] Umu ndi mmene Iye amalamulira mitundu ya anthu ndi kuwapatsa chakudya chochuluka.
[32] Amadzaza manja ake ndi zingʼaningʼani, ndipo amazilamulira kuti zigwe pamalo pamene Iye akufuna.
[33] Mabingu ake amalengeza za kubwera kwa mvula yamkuntho; ngʼombe nazo zimalengeza za kubwera kwake.