Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 4:47

[1] “Koma tsopano akundinyoza, ana angʼonoangʼono kwa ine, anthu amene makolo awo sindikanawalola kuti azithandizana ndi agalu anga kuweta nkhosa zanga.

[2] Kodi mphamvu zawo ndi za phindu lanji kwa ine, pakuti mphamvu zawo zinatha kale?

[3] Anali atatheratu kuwonda ndi njala, ankayendayenda mʼdziko lopanda madzi, mʼchipululu usiku.

[4] Ankathyola therere ndi masamba owawa, ndipo chakudya chawo chinali mizu ya mitengo ya masache.

[5] Anapirikitsidwa pakati pa anthu anzawo, akuwakuwiza ngati kuti anali akuba.

[6] Anawumirizidwa kukhala ku zigwembe za mitsinje yowuma, pakati pa matanthwe ndi mʼmaenje a mʼnthaka.

[7] Ankalira ngati nyama kuthengo ndipo ankawunjikana pamodzi pa ziyangoyango.

[8] Anali anthu achabechabe ndi wopanda dzina, anathamangitsidwa mʼdziko.

[9] “Ndipo tsopano ana awo akundiyimba nyimbo zachipongwe; ineyo ndasanduka chisudzo chawo.

[10] Iwo amanyansidwa nane ndipo amandithawa; akandiona salephera kundilavulira mʼmaso mwangamu.

[11] Tsopano pakuti Mulungu wakhwefula uta wanga ndipo wandisautsa, iwowo analekeratu kundiopa.

[12] Ku dzanja langa lamanja anthu akulimbana nane; andikumbira dzenje loti ndigweremo ndikamayenda, andipangira mitumbira ya nkhondo kuti alimbane nane.

[13] Iwo anditsekera njira; akufuna kundichititsa ngozi, popanda wina aliyense wowaletsa.

[14] Akundithamangitsa ngati madzi olowera pa mpanda wobowoka, iwo akubwererabwerera pakati pa chipasupasu.

[15] Zoopsa zandithetsa mphamvu; ulemu wanga wachita ngati wauluzika ndi mphepo, chuma changa chija chazimirira ngati mtambo.

[16] “Ndipo tsopano mtima wanga wachokamo; ndili mʼmasiku amasautso.

[17] Mafupa anga akuphwanya usiku pakuti zowawa zanga sizikuleka.

[18] Mʼmphamvu zake Mulungu wakhala ngati chovala changa; Iye wandigwira ngati chovala chondithina pa khosi.

[19] Wandiponya mʼmatope, ndipo ndasanduka ngati fumbi ndi phulusa.

[20] “Inu Mulungu, ine ndikulirira kwa Inu, koma simukundiyankha; ndikayimirira, Inu simundiyangʼana nʼkomwe.

[21] Inuyo mumandichitira zankhanza; mumandizunza ndi dzanja lanu lamphamvu.

[22] Mwandinyamulira ku mphepo ndipo mwandiwulutsa ndi mphepoyo; mwandiponya mʼmphepo ya mkuntho.

[23] Ndikudziwa kuti Inu mudzandifikitsa ku imfa, kumalo kumene amoyo onse adzapitako.

[24] “Ndithudi palibe munthu amene amalanga munthu wosweka mtima, amene akupempha thandizo mʼmasautso ake.

[25] Kodi ine sindinalire nawo iwo amene anali pamavuto? Kodi mtima wanga sunamvere chisoni anthu osauka?

[26] Koma pamene ndinkayembekezera zabwino, zoyipa ndiye zinandigwera; pamene ndinkafunafuna kuwala, mdima ndiye unandigwera.

[27] Kuwawa kwa mʼkati mwanga sikukuleka; ndili mʼmasiku amasautso.

[28] Ndikuyenda wothimbirira, komatu osati ndi dzuwa; ndimayimirira pa msonkhano ndi kupempha chithandizo molira.

[29] Ndasanduka mʼbale wa nkhandwe, mnzawo wa akadzidzi.

[30] Khungu langa layamba kuda ndipo likufunduka; thupi langa likutentha chifukwa cha kuphwanya kwa thupi.

[31] Pangwe wanga wasanduka woyimbira maliro, ndipo chitoliro changa chikuyimbira anthu olira.

Yobu — Chapters