[1] “Ndinachita pangano ndi maso anga kuti sindidzapenya namwali momusirira.
[2] Kodi Mulungu kumwambako wandisungira zotani? Kodi cholowa changa chochokera kwa Wamphamvuzonse kumwambako nʼchotani?
[3] Kodi si chiwonongeko kwa anthu oyipa, tsoka kwa iwo amene amachita zolakwa?
[4] Kodi Mulungu saona zochita zanga, ndi kudziwa mayendedwe anga?
[5] “Ngati ndachita zinthu mwachiphamaso, kapena kufulumira kukachita zachinyengo,
[6] Mulungu andiyeze ndi muyeso wake wolungama ndipo Iye adzadziwa kuti ine ndine wosalakwa,
[7] ngati mayendedwe anga asempha njira, ngati mtima wanga wakhumbira zimene maso anga aona, kapena ngati ndachita choyipa chilichonse.
[8] Pamenepo ena adye zimene ndinadzala, ndipo zomera zanga zizulidwe.
[9] “Ngati mtima wanga unakopekapo ndi mkazi, ndipo ngati ndinalakalaka mkazi wa mnansi wanga,
[10] pamenepo mkazi wanga aphikire mwamuna wina chakudya, ndipo amuna ena azigona naye.
[11] Pakuti zimenezo zikanakhala zochititsa manyazi, tchimo loyenera kulangidwa nalo.
[12] Ndi moto umene umayaka mpaka chiwonongeko; ukanapsereza zokolola zanga.
[13] “Ngati ndinkapondereza mlandu wa akapolo anga aamuna kapena aakazi, pamene ankabwera kwa ine ndi milandu yawo,
[14] ndidzatani pamene Mulungu adzanditsutsa? Nanga ndidzayankha chiyani akadzandifunsa?
[15] Kodi amene anapanga ine mʼmimba mwa amayi anga si yemwe anapanganso iwo? Kodi si mmodzi yemweyo amene anatipanga tonsefe mʼmimba mwa amayi athu?
[16] “Ngati ndinawamana aumphawi zinthu zimene ankazikhumba, kapena kuwagwiritsa fuwa lamoto akazi amasiye amene amafuna thandizo kwa ine,
[17] ngati chakudya changa ndinadya ndekha, wosagawirako mwana wamasiye,
[18] chonsechotu kuyambira unyamata wanga ndinamulera monga abambo ake, ndipo moyo wanga wonse ndakhala ndikusamalira akazi amasiye,
[19] ngati ndinaona wina aliyense akuzunzika ndi usiwa, kapena munthu wosauka alibe chofunda,
[20] ndipo ngati iyeyo sananditamandepo chifukwa chomufunditsa ndi nsalu ya ubweya wankhosa,
[21] ngati ndinaopsezapo mwana wamasiye, poganiza kuti ndinali ndi mphamvu mʼbwalo la milandu,
[22] pamenepo phewa langa lipokonyeke, mkono wanga ukonyoke polumikizira pake.
[23] Popeza ine ndinaopa kwambiri chiwonongeko chochokera kwa Mulungu, ndinachitanso mantha ndi ulemerero wake, sindikanatha kuchita zinthu zimenezi.
[24] “Ngati ndinayika mtima wanga pa chuma kapena kunena kwa golide wabwino kwambiri kuti, ‘Iwe ndiye chitetezo changa,’
[25] ngati ndinakondwera chifukwa choti chuma changa chinali chambiri, zinthu zimene manja anga anazipeza,
[26] ngati pamene ndinaona dzuwa likuwala, kapena mwezi ukuyenda mwa ulemerero wake,
[27] ndipo kuti mtima wanga unakopeka nazo nʼkuyika dzanja langa pakamwa mozilemekeza,
[28] pamenepo zimenezinso zikanakhala machimo oti ndilangidwe nawo, chifukwa ndikanakhala wosakhulupirika kwa Mulungu wakumwamba.
[29] “Ngati ndinasangalala ndi kuwonongeka kwa mdani wanga, kapena kusekera mavuto pamene mavuto anamugwera,
[30] ine sindinachimwe ndi pakamwa panga potulutsa matemberero a mdani wanga kuti awonongeke,
[31] ngati anthu amene ndimakhala nawo mʼnyumba mwanga sananenepo kuti, ‘Kodi ndani amene sakhuta ndi chakudya cha Yobu?’
[32] Komatu mlendo sindinamusiye pa msewu usiku wonse, pakuti khomo langa linali lotsekuka nthawi zonse kwa alendo,
[33] ngati ndinabisa tchimo langa monga amachitira anthu ena, kubisa kulakwa mu mtima mwanga
[34] chifukwa choopa gulu la anthu, ndi kuchita mantha ndi mnyozo wa mafuko kotero ndinakhala chete ndipo sindinatuluke panja.
[35] “Aa, pakanakhala wina wondimva! Tsopano ndikutsiriza mawu anga odzitetezera. Wamphamvuzonse andiyankhe; mdani wanga achite kulemba pa kalata mawu ake ondineneza.
[36] Ndithu ine ndikanakoleka kalatayo pa phewa langa, ndikanayivala kumutu ngati chipewa chaufumu.
[37] Ndikanamufotokozera zonse zimene ndinachita; ndikanafika pamaso pake ngati kalonga.
[38] “Ngati minda yanga ikulira monditsutsa ine ndipo malo ake onse osalimidwa anyowa ndi misozi,
[39] ngati ndinadya za mʼminda mwake osapereka ndalama kapena kukhumudwitsa anthu olima mʼmindamo,
[40] pamenepo mʼmindamo mumere namsongole mʼmalo mwa tirigu ndi udzu mʼmalo mwa barele.” Mawu a Yobu athera pano.