[1] “Chifukwa chiyani Wamphamvuzonse sayikiratu nthawi yoti aweruze? Chifukwa chiyani iwo amene amadziwa Iyeyo amayembekezera pachabe masiku oterewa?
[2] Anthu amasuntha miyala ya mʼmalire, kuti akuze dziko lawo; amadyetsa ziweto zimene aba.
[3] Amalanda abulu a ana amasiye ndipo amatenganso ngʼombe ya mkazi wamasiye ngati chikole.
[4] Amachotsa mʼmisewu anthu osauka, ndipo amathamangitsa amphawi onse mʼdziko.
[5] Amphawiwo amakhala ngati mbidzi mʼchipululu, amayendayenda kufuna chakudya; dziko lowuma limapereka chakudya cha ana awo.
[6] Iwo amakolola za mʼminda ya eni ake, ndipo amakunkha mphesa mʼminda ya anthu oyipa.
[7] Amagona maliseche usiku wonse kusowa zovala; pa nthawi yozizira amasowa chofunda.
[8] Amavumbwa ndi mvula ya mʼmapiri ndipo amakangamira ku matanthwe kusowa pobisalapo.
[9] Amatsomphola mwana wamasiye wa ku bere; ndipo amagwira mwana wakhanda wa mʼmphawi kuti akhale chikole.
[10] Amphawi amangoyenda maliseche kusowa zovala; amasenza mitolo ya tirigu, koma nʼkumagonabe ndi njala.
[11] Iwo amayenga mafuta a olivi mʼminda ya anthu oyipa; amapsinya mphesa, koma nʼkumamvabe ludzu.
[12] Kubuwula kwa anthu amene akufa kumamveka kuchokera mu mzinda, anthu ovulala akulirira chithandizo. Koma Mulungu sakuyimba mlandu wina aliyense.
[13] “Pali ena amene amakana kuwala, amene safuna kuyenda mʼkuwalako kapena kukhala mʼnjira zake.
[14] Dzuwa likalowa, wopha anzake amadzuka ndipo amakapha osauka ndi amphawi; nthawi ya usiku iye amasanduka mbala.
[15] Munthu wachigololo amadikira chisisira; iyeyo amaganiza kuti, ‘Palibe amene akundiona,’ ndipo amaphimba nkhope yake.
[16] Mbala zimathyola nyumba usiku, koma masana zimadzitsekera; izo zimathawa kuwala.
[17] Pakuti kwa onsewa mdima wandiweyani ndiye kuti kwawachera. Iwo amachita ubale ndi zoopsa za mdima.
[18] “Komatu iwowo ndi thovu loyandama pa madzi; minda yawo ndi yotembereredwa pa dzikolo kotero kuti palibe amene amapita ku minda ya mpesa.
[19] Monga momwe kutentha ndi chilala zimasungunulira madzi owundana ndi momwemonso mmene manda amachotsera omwe achimwa.
[20] Mayi wowabereka amawayiwala, mphutsi zimasangalala powadya; anthu oyipa sakumbukiridwanso koma amathyoka ngati mtengo.
[21] Amachitira nkhanza mayi wosabala ndi mayi amene alibe mwana, ndipo sakomera mtima mkazi wamasiye.
[22] Koma Mulungu amawononga munthu wamphamvu mwa mphamvu zake; ngakhale munthuyo atakhazikika, alibe chiyembekezo cha moyo wake.
[23] Mulungu atha kuwalola kuti akhale mosatekeseka, koma amakhala akupenyetsetsa njira zawo.
[24] Kwa kanthawi kochepa oyipa amakwezedwa ndipo kenaka saonekanso; amatsitsidwa ndipo amachotsedwa monga ena onse; amadulidwa ngati ngala za tirigu.
[25] “Ngati zimenezi sizoona, ndani angaonetse kuti ndine wabodza ndi kusandutsa mawu anga kukhala wopanda pake?”