Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 3:39

[1] “Ine ndatopa nawo moyo wanga; choncho ndidzanena zodandaula zanga momasuka ndipo ndidzayankhula mwa kuwawidwa mtima kwanga.

[2] Ndidzati kwa Mulungu wanga: Musandiweruze kuti ndine wolakwa, koma mundiwuze chifukwa chimene Inu mukukanganira ndi ine.

[3] Kodi mumakondwera mukamandizunza, kunyoza ntchito ya manja anu, chonsecho mukusekerera ndi zochita za anthu oyipa?

[4] Kodi maso anu ali ngati a munthu? Kodi mumaona zinthu monga momwe amazionera munthu?

[5] Kodi masiku anu ali ngati masiku a munthu, kapena zaka zanu ngati zaka za munthu,

[6] kuti Inu mufufuze zolakwa zanga ndi kulondola tchimo langa,

[7] ngakhale mukudziwa kuti sindine wolakwa ndiponso kuti palibe amene angandilanditse mʼdzanja lanu?

[8] “Munandiwumba ndi kundipanga ndi manja anu. Kodi tsopano Inu mudzatembenuka ndi kundiwononga?

[9] Kumbukirani kuti munandipanga ndi dothi, kodi tsopano mundibwezeranso ku fumbi?

[10] Suja munapatsa abambo anga mphamvu zoti andibale, suja munandikuza bwino mʼmimba mwa amayi anga?

[11] Munandikuta ndi khungu ndi mnofu ndi kundilumikiza pamodzi ndi mafupa ndi mitsempha?

[12] Munandipatsa moyo ndi kundionetsa chifundo chanu, ndipo munasamalira bwino moyo wanga.

[13] “Koma izi ndi zimene munabisa mu mtima mwanu, ndipo ndikudziwa kuti zinali mʼmaganizo anu:

[14] Kuti ngati ndingachimwe mudzakhala mukundipenyetsetsa ndipo kuti simudzalola kuti ndisalangidwe chifukwa cha kulakwa kwanga.

[15] Ngati ndili wolakwa, tsoka langa! Koma ngakhale ndili wosalakwa sindingathe kutukula mutu wanga, pakuti ndagwidwa ndi manyazi ndipo ndamizidwa mʼmavuto anga.

[16] Ndipo ndikatukula mutu wanga, Inu mumandisaka ngati mkango ndiponso mumandiopseza ndi mphamvu yanu.

[17] Mumabweretsa mboni zatsopano potsutsana nane ndipo mkwiyo wanu pa ine umanka nukulirakulira ndi magulu anu olimbana nane amanka nachulukirachulukira.

[18] “Chifukwa chiyani Inu munalola kuti ndibadwe? Ndi bwino ndikanafa diso lililonse lisanandione.

[19] Ndikanapanda kubadwa, kapena akanangonditenga nditabadwa kupita nane ku manda!

[20] Kodi masiku anga owerengeka sali pafupi kutha? Ndilekeni kuti ndipumule pangʼono pokha

[21] ndisanapite ku malo amene munthu sabwererako ku dziko la imfa ndi kwa mdima wandiweyani,

[22] ku dziko la mdima wandiweyani ndi chisokonezo, kumene kuwala kumakhala ngati mdima.”

Yobu — Chapters