[1] Pamenepo Elifazi wa ku Temani anayankha kuti,
[2] “Kodi munthu wanzeru angayankhe ndi mawu achabechabe otere, kapena angakhutitse mimba yake ndi mphepo yotentha yochokera kummawa?
[3] Kodi angathe kutsutsa ndi mawu opanda pake, kapena kuyankhula mawu opanda phindu?
[4] Koma iwe ukuchepetsa zoopa Mulungu ndipo ukutchinga zodzikhuthulira kwa Mulungu.
[5] Tchimo lako ndiye likuyankhulitsa pakamwa pakopo; ndipo watengera mayankhulidwe a atambwali.
[6] Pakamwa pakopo ndiye pakukutsutsa osati pakamwa panga; milomo yakoyo ikukutsutsa.
[7] “Kodi ndiwe munthu woyamba kubadwa? Kodi unalengedwa mapiri asanalengedwe?
[8] Kodi unali mʼgulu la alangizi a Mulungu? Kodi ukudziyesa wanzeru ndiwe wekha?
[9] Kodi iwe umadziwa chiyani chimene ife sitichidziwa? Kodi iwe uli ndi chidziwitso chanji chimene ife tilibe?
[10] Anthu a imvi ndi okalamba ali mbali yathu, anthu amvulazakale kupambana abambo ako.
[11] Kodi mawu otonthoza mtima ochokera kwa Mulungu sakukukwanira, mawu oyankhula mofatsawa kwa iwe?
[12] Chifukwa chiyani ukupsa mtima, ndipo chifukwa chiyani ukutuzula maso ako,
[13] moti ukupsera mtima Mulungu ndi kuyankhula mawu otero pakamwa pako?
[14] “Kodi munthu nʼchiyani kuti nʼkukhala woyera mtima kapena wobadwa mwa amayi nʼchiyani kuti nʼkukhala wolungama mtima?
[15] Ngati Mulungu sakhulupirira ngakhale angelo ake, ngakhale zakumwamba sizoyera pamaso pake,
[16] nanga kuli bwanji munthu amene ndi wonyansa ndi wa njira zokhotakhota, amene kuchita zoyipa kuli ngati kumwa madzi.
[17] “Mvetsera kwa ine ndipo ndidzakufotokozera; ndilole ndikuwuze zimene ndaziona,
[18] zimene anandiphunzitsa anthu anzeru, sanandibisire kalikonse kamene anamva kuchokera kwa makolo awo.
[19] (Ndi kwa iwowa kumene dziko lino linaperekedwa pamene panalibe mlendo wokhala pakati pawo).
[20] Munthu woyipa amavutika ndi masautso masiku onse a moyo wake, munthu wankhanza adzavutika zaka zake zonse.
[21] Amamva mawu owopsa mʼmakutu mwake, pamene zonse zikuoneka ngati zili bwino, anthu achifwamba amamuthira nkhondo.
[22] Iye sakhulupirira kuti angathe kupulumuka ku mdima wa imfa; iyeyo ndi woyenera kuphedwa.
[23] Amangoyendayenda pali ponse kunka nafuna chakudya; amadziwa kuti tsiku la mdima lili pafupi.
[24] Masautso ndi nthumanzi zimamuchititsa mantha kwambiri; zimamugonjetsa iye monga imachitira mfumu yokonzekera kukathira nkhondo,
[25] chifukwa iye amatambasula dzanja lake kuyambana ndi Mulungu ndipo amadzitama yekha polimbana ndi Wamphamvuzonse.
[26] Amapita mwa mwano kukalimbana naye atanyamula chishango chochindikala ndi cholimba.
[27] “Ngakhale nkhope yake ndi yonenepa ndipo mʼchiwuno mwake muli mnofu wambiri,
[28] munthuyo adzakhala mʼmizinda yowonongeka ndi mʼnyumba zosayenera kukhalamo anthu, nyumba zimene zikugwa ndi kuwonongeka.
[29] Iye sadzalemeranso ndipo chuma chake sichidzakhalitsa, ngakhale minda yake sidzabala zipatso pa dziko lapansi.
[30] Iyeyo sadzapulumuka mu mdimamo; lawi lamoto lidzawumitsa nthambi zake, ndipo mpweya wochokera mʼkamwa mwa Mulungu udzamusesa.
[31] Asadzinyenge yekha podalira zinthu zachabechabe, pakuti pa mapeto pake sadzaphulapo kanthu.
[32] Iye adzalandira malipiro ake nthawi yake isanakwane, ndipo nthambi zake sizidzaphukanso.
[33] Iye adzakhala ngati mtengo wamphesa wopululidwa zipatso zake zisanapse, adzakhala ngati mtengo wa olivi umene wayoyola maluwa ake.
[34] Pakuti anthu osapembedza Mulungu adzakhala osabala ndipo moto udzapsereza nyumba za onse okonda ziphuphu.
[35] Iwo amalingalira zaupandu ndipo amachita zoyipa; mtima wawo umakonzekera zachinyengo.”