[1] Apo Yehova anamuyankha Yobu mʼkamvuluvulu. Ndipo anati:
[2] “Kodi uyu ndani amene akusokoneza uphungu wanga poyankhula mawu opanda nzeru?
[3] Onetsa chamuna; ndikufunsa ndipo undiyankhe.
[4] “Kodi unali kuti pamene ndinkayika maziko a dziko lapansi? Ndiwuze ngati ukudziwa.
[5] Ndani amene analemba malire ake? Ndithudi iwe ukudziwa! Ndani amene anayeza ndi chingwe dzikoli?
[6] Kodi maziko ake anawakumba potani, kapena ndani anayika mwala wake wapangodya,
[7] pamene nyenyezi za kummawa zinkayimba pamodzi ndipo angelo onse a Mulungu ankafuwula mokondwa?
[8] “Kodi ndani amene anatsekera nyanja pamene inkalengedwa, pamene inkachita ngati kutumphuka pansi pa dziko,
[9] pamene ndinasandutsa mitambo kukhala chovala chake ndi kuyikulunga mu mdima wandiweyani,
[10] pamene ndinayilembera malire ake ndikuyikira zitseko ndi mipiringidzo yake.
[11] Pamene ndinati, ‘Ufike mpaka apa ndipo usapitirire apa ndiye pamene mafunde ako amphamvuwo azilekezera?’
[12] “Kodi chibadwire chako unalamulapo dzuwa kuti lituluke mmawa, kapena kuti mʼbandakucha ukhalepo pa nthawi yake,
[13] kuti kuwalako kuwunikire dziko lonse lapansi ndi kuthamangitsa anthu oyipa?
[14] Chifukwa cha kuwala kwa usana mapiri ndi zigwa zimaonekera bwino ngati zilembo za chidindo pa mtapo; zimaonekera bwino ngati makwinya a chovala.
[15] Kuwala kwa dzuwako sikuwafikira anthu oyipa, ndipo dzanja lawo silingathe kuchita kanthu.
[16] “Kodi unayendapo pansi penipeni pa nyanja kapena pa magwero ake ozama?
[17] Kodi anakuonetsapo zipata za imfa? Kodi unaonako ku dziko la anthu akufa kumene kuli mdima wandiweyani?
[18] Kodi kukula kwa dziko lapansi umakudziwa? Undiwuze ngati ukuzidziwa zonsezi.
[19] “Kodi njira yopita kumene kumakhala kuwala ili kuti? Nanga mdima umakhala kuti?
[20] Kodi iwe ungathe kuziperekeza kwawoko zimenezi? Kodi ukuyidziwa njira yopita kwawoko?
[21] Ndithu, iwe ukuyidziwa, poti paja nthawi imeneyo nʼkuti utabadwa kale! Wakhala ndi moyo zaka zambiridi!
[22] “Kodi unalowamo mʼnyumba zosungira chisanu chowundana kapena unayionapo nyumba yosungira matalala,
[23] zimene ndazisungira nthawi ya mavuto ndi nthawi yomenyana ndi ya nkhondo?
[24] Kodi umadziwa njira ya kumene kumachokera chingʼaningʼani kapena njira ya kumene kumachokera mphepo ya kummawa imene ili pa dziko lonse lapansi?
[25] Kodi ndani amene amakonza ngalande za mvula, nanga ndani anakonza njira yoyendamo mphenzi,
[26] kuthirira madzi dziko limene sikukhala munthu, chipululu chopandamo munthu,
[27] kukhutitsa nthaka yowuma yagwaa ndi kumeretsamo udzu?
[28] Kodi mvula ili ndi abambo ake? Nanga madzi a mame anawabereka ndani?
[29] Kodi madzi owundana anawabereka ndani? Ndani amene anabereka chisanu chochokera kumwamba
[30] pamene madzi amawuma gwaa ngati mwala, pamene madzi a pa nyanja amazizira, nalimba kuti gwaa?
[31] “Kodi iwe ungayimitse kuyenda kwa nyenyezi? Kodi ungathe kuletsa kuyenda kwa nsangwe ndi akamwiniatsatana?
[32] Kodi ungathe kuwongolera nyenyezi pa nyengo yake kapena kutsogolera nyenyezi yayikulu ya chimbalangondo pamodzi ndi ana ake?
[33] Kodi malamulo a mlengalenga umawadziwa? Kodi ungathe kukhazikitsa ulamuliro wa Mulungu pa dziko lapansi?
[34] “Kodi iwe ungathe kulamula mitambo kuti igwetse mvula ya chigumula?
[35] Kodi ungathe kutumiza zingʼaningʼani kuti zingʼanime? Kodi zimabwera pamaso pako ndi kuti, ‘Tili pano?’
[36] Kodi ndani anayika nzeru mu mtima, ndani analonga mʼmaganizo nzeru zomvetsa zinthu?
[37] Wanzeru ndani amene angathe kuwerenga mitambo? Ndani angathe kupendeketsa mitsuko ya madzi akuthambo
[38] pamene fumbi limasanduka matope, ndipo matopewo amawumbika?
[39] “Kodi ndani amawusakira chakudya mkango waukazi ndi kukhutitsa misona ya mikango
[40] pamene ili khale mʼmapanga mwawo kapena pamene ikubisala pa tchire?
[41] Kodi amamupatsa khwangwala chakudya chake ndani pamene ana ake akulirira kwa Mulungu ndi kumayendayenda chifukwa chosowa zakudya?