Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 3:40

[1] Pamenepo Yobu anayankha kuti,

[2] “Ndinamvapo zambiri monga zimenezi; nonsenu ndinu anthu osatha kutonthoza mtima mnzanu.

[3] Kodi mawu anu ochulukawo adzatha? Kodi chikukuvutani nʼchiyani kuti muzingoyankhula mawu otsutsawa?

[4] Inenso ndikanatha kuyankhula monga inu, inuyo mukanakhala monga ndilili inemu; Ine ndikanatha kuyankhula mawu omveka bwino kutsutsana nanu ndi kukupukusirani mutu wanga.

[5] Ndipo mawu a pakamwa panga akanakulimbikitsani; chitonthozo chochokera pa milomo yanga chikanachepetsa ululu wanu.

[6] “Koma ine ndikati ndiyankhule ululu wanga sukuchepa; ndipo ndikati ndikhale chete, ululu wanga sukuchokabe.

[7] Ndithudi, Inu Mulungu mwanditha mphamvu; mwawononga banja langa lonse.

[8] Inu mwandimanga ndipo kundimangako kwakhala umboni; kuwonda kwanga kwandiwukira ndipo kukuchita umboni wonditsutsa.

[9] Mulungu amabwera kwa ine mwankhanza ndipo amadana nane, amachita kulumira mano; mdani wanga amandituzulira maso.

[10] Anthu amatsekula pakamwa pawo kundikuwiza; amandimenya pa tsaya mwachipongwe ndipo amagwirizana polimbana nane.

[11] Mulungu wandipereka kwa anthu ochita zoyipa ndipo wandiponyera mʼmanja mwa anthu oyipa mtima.

[12] Ine ndinali pamtendere, koma Mulungu ananditswanya; anandigwira pa khosi ndi kundiphwanya. Iye anandisandutsa choponyera chandamale chake;

[13] anthu ake oponya mauta andizungulira. Mopanda kundimvera chisoni, Iye akulasa impsyo zanga ndipo akutayira pansi ndulu yanga.

[14] Akundivulaza kawirikawiri, akuthamangira pa ine monga munthu wankhondo.

[15] “Ndasokerera chiguduli pa thupi langa ndipo ndayika mphamvu zanga pa fumbi.

[16] Maso anga afiira ndi kulira, ndipo zikope zanga zatupa;

[17] komatu manja anga sanachite zachiwawa ndipo pemphero langa ndi lolungama.

[18] “Iwe dziko lapansi, usakwirire magazi anga; kulira kwanga kofuna thandizo kusalekeke!

[19] Ngakhale tsopano mboni yanga ili kumwamba; wonditchinjiriza pa mlandu wanga ali komweko.

[20] Wondipembedzera ndi bwenzi langa, pamene maso anga akukhuthula misozi kwa Mulungu;

[21] iye, mʼmalo mwanga, amamudandaulira Mulungu monga munthu amadandaulira bwenzi lake.

[22] “Pakuti sipapita zaka zambiri ndisanayende mʼnjira imene sindidzabwerera.”

Yobu — Chapters