Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 0:49

[1] Apo Bilidadi wa ku Suki anayankha kuti,

[2] “Ulamuliro ndi kuopsa ndi za Mulungu, Iye amakhazikitsa bata mu ufumu wake kumwambako.

[3] Kodi magulu ake ankhondo nʼkuwerengeka? Kodi kuwala kwake sikuwalira ndani?

[4] Kodi munthu angakhale bwanji wolungama pamaso pa Mulungu? Kodi munthu wobadwa mwa mayi angakhale wangwiro?

[5] Ngati mwezi sutha kuwala kwenikweni, ndipo nyenyezi sizitha kuwala pamaso pake,

[6] nanji tsono munthu amene ali ngati mphutsi, mwana wa munthu amene ali ngati nyongolotsi!”

Yobu — Chapters