Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 4:07

[1] Pamenepo Yobu anayankha kuti,

[2] “Ndithudi inuyo ndinu anthu ndipo nzeru zanu zidzafera nanu pamodzi!

[3] Koma inenso ndili nazo nzeru ngati inu; ineyo sindine munthu wamba kwa inu. Ndani amene sadziwa zonse zimene mwanenazi?

[4] “Ndasanduka chinthu choseketsa kwa abwenzi anga, ngakhale ndinkapemphera kwa Mulungu ndipo Iye ankandiyankha. Ine ndasanduka chinthu chongoseketsa, ngakhale ndili wolungama ndi wosalakwa!

[5] Anthu amene ali pabwino amanyoza anzawo amene ali pa tsoka. Tsokalo limagwa pa amene wayamba kale kugwa.

[6] Nyumba za anthu achifwamba zimakhala pa mtendere, ndipo anthu amene amaputa Mulungu amakhala pabwino, amene amanyamula milungu yawo mʼmanja.

[7] “Koma funsa nyama zakuthengo ndipo zidzakuphunzitsa, kapena mbalame zamumlengalenga ndipo zidzakuwuza;

[8] kapena uyankhule ndi dziko lapansi ndipo lidzakuphunzitsa, kapena ulole nsomba zamʼnyanja kuti zikufotokozere.

[9] Kodi mwa zonsezi ndi chiti chimene sichidziwa kuti lachita zimenezi ndi dzanja la Yehova?

[10] Mʼmanja mwake ndi mʼmene muli moyo wa cholengedwa chilichonse, ndiponso moyo wa anthu a mitundu yonse.

[11] Kodi khutu sindiye limene limamva mawu monga mmene lilime limalawira chakudya?

[12] Kodi nzeru sipezeka pakati pa anthu okalamba? Kodi moyo wautali sumabweretsa nzeru zomvetsa zinthu?

[13] “Kwa Mulungu ndiye kuli nzeru ndi mphamvu; uphungu ndi kumvetsa zinthu ndi zake.

[14] Chimene Iye wapasula palibe angachimangenso. Akatsekera munthu mʼndende palibe angamutulutse.

[15] Iyeyo akamanga mvula dziko limawuma; akamasula mvulayo, madzi amasefukira pa dziko.

[16] Kwa Iye kuli mphamvu ndi kupambana; munthu wopusitsidwa ndiponso wopusitsa onse ali mu ulamuliro wake.

[17] Iye amalanda aphungu nzeru zawo ndipo amapusitsa oweruza.

[18] Iye amachotsa zingwe zimene mafumu anawamanga nazo ndipo amawamanga lamba mʼchiwuno mwawo.

[19] Iye amasocheretsa ansembe atawalanda nzeru zawo ndipo amagonjetsa anthu amphamvu amene ndi okhazikika.

[20] Iye amakhalitsa chete aphungu odalirika ndipo amalanda chidziwitso cha anthu akuluakulu.

[21] Iye amanyoza anthu otchuka ndipo anthu anyonga amawatha mphamvu.

[22] Iye amatulutsira poyera zinthu zozama za mu mdima ndipo mdima wandiweyaniwo amawusandutsa kuwala.

[23] Iye amakuza mitundu ya anthu ndipo amayiwononganso; amachulukitsa mitundu ya anthu ndipo amayimwazanso.

[24] Iye amalanda nzeru za atsogoleri a dziko lapansi; amawayendetsa mʼthengo mopanda njira.

[25] Iwo amafufuzafufuza njira mu mdima wopanda chowunikira; Iye amawayendetsa dzandidzandi ngati oledzera.

Yobu — Chapters