Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 5:29

[1] Pamenepo Elihu anapitiriza kuyankhula kuti,

[2] “Imvani mawu anga, inu anthu anzeru; tcherani khutu inu anthu ophunzira.

[3] Pakuti khutu limayesa mawu monga momwe mʼkamwa mumalawira chakudya.

[4] Tsono tiyeni tizindikire chomwe chili choyenera; tiphunzire pamodzi chomwe chili chabwino.

[5] “Yobu akunena kuti, ‘Ndine wosalakwa, koma Mulungu akukana kundiweruza molungama.

[6] Ngakhale ndine wolungama mtima, akundiyesa wabodza; ngakhale ndine wosachimwa, mivi yake ikundichititsa mabala osachiritsidwa.’

[7] Kodi munthu wofanana ndi Yobu ndani, amene amayankhula zamwano ngati akumwa madzi?

[8] Iye amayenda ndi anthu ochita zoyipa; amayanjana ndi anthu oyipa mtima.

[9] Paja iye amanena kuti, ‘Munthu sapindula kanthu poyesetsa kukondweretsa Mulungu.’

[10] “Tsono mverani ine, inu anthu anzeru zomvetsa zinthu. Mulungu sangachite choyipa ndi pangʼono pomwe, Wamphamvuzonse sangathe kuchita cholakwa.

[11] Iye amamubwezera munthu molingana ndi ntchito zake; Mulungu amabweretsa pa munthu molingana ndi zomwe amachita.

[12] Nʼchosayembekezeka kuti Mulungu achite cholakwa, kuti Wamphamvuzonse apotoze chilungamo.

[13] Kodi anapatsa Mulungu udindo wolamulira dziko lapansi ndani? Ndani anayika Mulungu kuti azilamulira dziko lonse?

[14] Mulungu akanakhala ndi maganizo oti achotse mzimu wake ndi mpweya wake,

[15] zamoyo zonse zikanawonongekeratu ndipo munthu akanabwerera ku fumbi.

[16] “Ngati ndinu omvetsa zinthu, imvani izi; mvetserani zimene ndikunena.

[17] Kodi Mulungu wodana ndi chilungamo angathe kukhala wolamulira? Kodi iwe ungathe kuweruza Wolungama ndi Wamphamvuyo?

[18] Kodi si Iye amene amanena kwa mafumu kuti, ‘Ndinu opanda pake,’ ndipo amawuza anthu otchuka, ‘Ndinu oyipa,’

[19] Iye sakondera akalonga ndipo salemekeza anthu olemera kupambana osauka, pakuti onsewa ndi ntchito ya manja ake?

[20] Iwo amafa mwadzidzidzi, pakati pa usiku; anthu amachita mantha ndipo amamwalira; munthu wamphamvu amachotsedwa popanda dzanja la munthu.

[21] “Maso a Mulungu amapenya njira za munthu; amaona mayendedwe ake onse.

[22] Palibe malo obisika kapena a mdima wandiweyani kumene anthu ochita zoyipa angabisaleko.

[23] Mulungu sasowa kuti apitirizebe kufufuza munthu, kuti abwere pamaso pake kudzaweruzidwa.

[24] Popanda kufufuza, Iye amawononga anthu amphamvu ndipo mʼmalo mwawo amayikamo ena.

[25] Pakuti Iyeyo amadziwa bwino ntchito zawo amawagubuduza usiku ndipo amatswanyika.

[26] Iye amawalanga chifukwa cha kuyipa kwawo, pamalo pamene aliyense akuwaona;

[27] Chifukwa anasiya kumutsata ndipo sasamaliranso njira zake zonse.

[28] Anachititsa amphawi kuti kulira kwawo kufike pamaso pake, kotero Iyeyo anamva kulira kwa amphawiwo.

[29] Koma ngati Mulungu akhala chete, ndani angamunene kuti walakwa? Akabisa nkhope yake, ndani angathe kumupenyabe? Komatu ndiye amene amayangʼana za munthu komanso mtundu wa anthu,

[30] kuti asalamuliridwe ndi anthu osapembedza, kuti asatchere anthu misampha.

[31] “Mwina munthu atanena kwa Mulungu kuti, ‘Ndine wolakwa koma sindidzachimwanso,

[32] ndiphunzitseni zimene sindikuziona ngati ndachita choyipa, sindidzachitanso.’

[33] Kodi Mulungu akuweruzeni potsata mmene inuyo mukuganizira, pamene inu mukukana kulapa? Chisankho nʼchanu, osati changa; tsono ndiwuzeni zomwe mukudziwa.

[34] “Anthu omvetsa zinthu adzakambirana, anthu anzeru amene akundimva adzandiwuza kuti,

[35] ‘Yobu akuyankhula mopanda nzeru; mawu ake ndi opanda fundo.’

[36] Aa, kunali bwino Yobu akanayesedwa mpaka kumapeto chifukwa choyankha ngati munthu woyipa!

[37] Pa tchimo lake amawonjezerapo kuwukira; amawomba mʼmanja mwake monyoza pakati pathu, ndipo amachulukitsa mawu otsutsana ndi Mulungu.”

Yobu — Chapters