[1] Pambuyo pake Yobu anatsekula pakamwa pake nayamba kutemberera tsiku limene iyeyo anabadwa.
[2] Ndipo Yobu anati:
[3] “Tsiku limene ine ndinabadwa litembereredwe ndi usiku umene ananena kuti, ‘Mwana wamwamuna wabadwa!’
[4] Tsiku limenelo lisanduke mdima; Mulungu wa kumwambako asalilabadirenso; kuwala kusaonekenso pa tsikulo.
[5] Mdima ndi mthunzi wa imfa zikhale pa tsiku limeneli; mtambo uphimbe tsikuli; mdima wandiweyani udetse kuwala kwake.
[6] Usiku umenewo ukutidwe ndi mdima wandiweyani; usawerengedwenso pamodzi ndi masiku a chaka, kapena kukhala pa mwezi wina uliwonse.
[7] Usiku umenewo usabweretse chilichonse chabwino; kusamvekenso nthungululu za chikondwerero.
[8] Odziwa kutemberera masiku alitemberere tsikulo, iwo amene akonzekera kuwutsa Leviyatani.
[9] Nyenyezi zake za mʼbandakucha zikhale mdima; tsikulo liyembekezere kucha pachabe ndipo lisaonenso kuwala koyamba kwa mʼbandakucha.
[10] Pakuti tsiku limenelo ndiye ndinatuluka mʼmimba ya amayi anga ndipo ndi limene linandionetsa zovuta.
[11] “Bwanji ine sindinawonongeke pamene ndinkabadwa ndi kufa pamene ndimatuluka mʼmimba?
[12] Chifukwa chiyani panali mawondo wondilandirirapo ndi mawere woti andiyamwitsepo?
[13] Pakuti tsopano bwenzi ndili gone mwamtendere; ndikanakhala nditagona tulo ndili pa mpumulo
[14] pamodzi ndi mafumu ndi aphungu a dziko lapansi, amene anadzimangira nyumba zikuluzikulu zimene tsopano ndi mabwinja,
[15] pamodzi ndi olamulira amene anali ndi golide, amene anadzaza nyumba zawo ndi siliva.
[16] Kapena, bwanji sindinakwiriridwe pansi monga mwana wobadwa wakufa kale, ngati khanda limene silinaone kuwala kwa dzuwa?
[17] Ku mandako anthu oyipa sakhalanso pa mavuto, ndipo kumeneko anthu otopa ali pa mpumulo.
[18] A mʼndende kumeneko akusangalala ndi mtendere; sakumvanso mawu ofuwula a kapitawo wa akapolo.
[19] Anthu wamba ndi anthu apamwamba ali kumeneko, ndipo kapolo ndi womasuka kwa mbuye wake.
[20] “Chifukwa chiyani dzuwa limawalira iwo amene ali pa mavuto, ndipo moyo umapatsidwa kwa owawidwa mtima,
[21] kwa iwo amene amalakalaka imfa imene sibwera, amene amayifunafuna imfayo kupambana chuma chobisika,
[22] amene amakondwa ndi kusangalala akamalowa mʼmanda?
[23] Chifuwa chiyani moyo umaperekedwa kwa munthu amene njira yake yabisika, amene Mulungu wamuzinga ponseponse?
[24] Mʼmalo moti ndidye, ndimalira, ndi kubuwula kwanga nʼkosalekeza.
[25] Chimene ndinkachiopa chandigwera; chimene ndinkachita nacho mantha chandichitikira.
[26] Ndilibe mtendere kapena bata, ndilibe mpumulo, koma mavuto okhaokha.”