Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 5:20

[1] Pamenepo Yobu anayankha kuti,

[2] “Mvetserani bwino mawu anga; ichi chikhale chitonthozo changa chochokera kwa inu.

[3] Ndiloleni ndiyankhule ndipo ndikatha kuyankhula munditonzetonze.

[4] “Kodi ine ndikudandaulira munthu? Tsono ndilekerenji kupsa mtima?

[5] Ndipenyeni ndipo mudabwe; mugwire dzanja pakamwa.

[6] Ndikamaganiza zimenezi ndimachita mantha kwambiri; thupi langa limanjenjemera.

[7] Chifukwa chiyani anthu oyipa amakhalabe ndi moyo, amakalamba ndi kusanduka amphamvu?

[8] Amaona ana awo akukhazikika pamodzi nawo, zidzukulu zawo zikukula bwino iwo akuona.

[9] Mabanja awo amakhala pa mtendere ndipo sakhala ndi mantha; mkwapulo wa Mulungu suwakhudza nʼkomwe.

[10] Ngʼombe zawo zazimuna sizilephera kubereketsa; ngʼombe zawo zazikazi sizipoloza.

[11] Amatulutsa ana awo ngati gulu la nkhosa; makanda awo amavinavina pabwalo.

[12] Amayimba nyimbo pogwiritsa ntchito matambolini ndi azeze; amakondwa pakumva kulira kwa chitoliro.

[13] Zaka zawo zimatha ali mu ulemerero ndipo amatsikira ku manda mwamtendere.

[14] Koma anthuwo amawuza Mulungu kuti, ‘Tichokereni!’ Ife tilibe chikhumbokhumbo chofuna kudziwa njira zanu.

[15] Kodi Wamphamvuzonseyo ndani kuti timutumikire? Ife tipindula chiyani tikamapemphera kwa Iyeyo?

[16] Komatu ulemerero wawo suli mʼmanja mwawo, koma ine ndimakhala patali ndi uphungu wa anthu oyipa.

[17] “Koma nʼkangati kamene nyale ya anthu oyipa imazimitsidwa? Nʼkangati kamene tsoka limawagwera? Nʼkangati kamene Mulungu amawakwiyira ndi kuwalanga?

[18] Nʼkangati kamene iwo amakhala ngati phesi lowuluka ndi mphepo, ngati mungu wowuluzika ndi kamvuluvulu?

[19] Paja amati, ‘Mulungu amalanga ana chifukwa cha machimo abambo awo.’ Koma Mulungu amabwezera chilango munthuyo, kuti adziwe kuti Mulungu amalangadi.

[20] Mulole kuti adzionere yekha chilango chake, kuti alawe ukali wa Wamphamvuzonse.

[21] Nanga kodi amalabadira chiyani zabanja lake limene walisiya mʼmbuyo, pamene chiwerengero cha masiku ake chatha?

[22] “Kodi alipo wina amene angaphunzitse Mulungu nzeru, poti Iye amaweruza ngakhale anthu apamwamba?

[23] Munthu wina amamwalira ali ndi mphamvu zonse, ali pa mtendere ndi pa mpumulo,

[24] thupi lake lili lonenepa, mafupa ake ali odzaza ndi mafuta.

[25] Munthu wina amamwalira ali wowawidwa mtima, wosalawapo chinthu chabwino chilichonse.

[26] Olemera ndi osauka omwe amamwalira ndi kuyikidwa mʼmanda ndipo onse amatuluka mphutsi.

[27] “Ndikudziwa bwino zimene mukuganiza, ziwembu zanu zomwe mukuti mundichitire.

[28] Inu mukuti, ‘Kodi nyumba ya mkulu uja ili kuti, matenti amene munkakhala anthu oyipa aja ali kuti?’

[29] Kodi munawafunsapo anthu amene ali pa ulendo? Kodi munaganizirapo zimene iwo amanena?

[30] Zakuti munthu woyipa amasungidwa chifukwa cha tsiku la tsoka, kuti amapulumutsidwa chifukwa cha tsiku la ukali wa Mulungu?

[31] Kodi ndani amadzudzula munthu wochimwayo? Ndani amamubwezera zoyipa zimene anachita?

[32] Iye amanyamulidwa kupita ku manda ndipo anthu amachezera pa manda ake.

[33] Dothi la ku chigwa limamukomera; anthu onse amatsatira mtembo wake, ndipo anthu osawerengeka amakhala patsogolo pa chitanda chakecho.

[34] “Nanga inu mudzanditonthoza bwanji ine ndi mawu anu opandapakewo palibe chimene chatsala kuti muyankhe koma mabodza basi!”

Yobu — Chapters