[1] Pali mgodi wa siliva ndiponso malo oyengerapo golide.
[2] Chitsulo amachikumba pansi, ndipo mkuwa amawusungunula ku miyala yamkuwa.
[3] Munthu amalowa mu mdima atatenga nyale, amafunafuna miyala mpaka ku malire a mgodiwo, kufuna mkuwa mu mdima wandiweyani.
[4] Amakumba njira zapansi mu mgodimo, kutali ndi kumene kumakhala anthu, kumalo kumene phazi la munthu silinapondeko; iye amakhala ali lende pansipo namazungulira uku ndi uku.
[5] Nthaka, imene imatulutsa zakudya, kunsi kwake kumachita ngati kwasandulizika ndi moto;
[6] miyala ya safiro imachokera mʼmatanthwe ake, ndipo mʼfumbi lake mumakhala miyala yagolide.
[7] Palibe mbalame yodya zinzake imene imadziwa njira yobisikayi, palibe kamtema amene anayiona.
[8] Zirombo zolusa sizipondamo mʼnjiramo, ndipo mkango sudzeranso mʼmenemo.
[9] Munthu amaphwanya matanthwe olimba, ndipo amagubuduza mapiri kuyambira mʼtsinde.
[10] Amabowola njira mʼmatanthwewo; ndipo amaona chuma chonse cha mʼphirimo.
[11] Amaletsa mitsinje ya pansipo kuti isayendenso, motero amatulutsira poyera zinthu zobisika.
[12] “Koma nzeru zingapezeke kuti? Kodi kumvetsa zinthu kumakhala kuti?
[13] Munthu sadziwa kufunika kwake kwa nzeruzo; nzeruyo sipezeka pa dziko lino la anthu amoyo.
[14] Phompho likuti, ‘Sizipezeka mwa ine muno.’ Nyanja ikuti, ‘Mwa ine munonso ayi.’
[15] Nzeru sungazigule ndi golide wabwino kwambiri, mtengo wake sungawuyerekeze ndi siliva wambiri.
[16] Nzeru singagulidwe ndi golide wa ku Ofiri, kapena ndi miyala ya onikisi kapena ya safiro.
[17] Nzeru sungayiyerekeze ndi golide kapena mwala wa galasi, sungayigule ndi zokometsera zagolide.
[18] Miyala ya korali ndi krisitali siyoyeneranso ndi kuyitchula nʼkomwe; mtengo wa nzeru ndi woposa miyala ya rubi.
[19] Nzeru sungayiyerekeze ndi miyala ya topazi ya ku Kusi; nzeru singagulidwe ndi golide wabwino kwambiri.
[20] “Kodi tsono nzeru zimachokera kuti? Kodi kumvetsa zinthu kumakhala kuti?
[21] Malo ake ndi obisika kwa zamoyo zonse, ndi obisika ngakhale kwa mbalame zamlengalenga.
[22] Chiwonongeko ndi imfa zikuti, ‘Tangomva mphekesera chabe ya zimenezo!’
[23] Mulungu yekha ndiye amadziwa njira yake yopita kumeneko, ndipo Iye yekha amadziwa kumene nzeru imakhala,
[24] pakuti Iye amayangʼana mpaka ku malekezero a dziko lapansi ndipo amaona zonse za kunsi kwa thambo.
[25] Iye atapatsa mphepo mphamvu zake, nayeza kuzama kwa nyanja,
[26] atakhazikitsa lamulo loti mvula izigwa ndi kukonza njira ya chingʼaningʼani cha bingu,
[27] pamenepo ndi pamene anayangʼana nzeruzo naziyeza mtengo wake; nazikhazikitsa ndi kuzisanthula bwino lomwe.
[28] Ndipo Iye anati kwa munthu, ‘Taonani, kuopa Ambuye, ndiye nzeru zimenezo ndipo kuthawa zoyipa ndiye kumvetsa zinthu kumeneko.’ ”