Skip to content
Opens in a new window
Listen to this chapter • 4:24

[1] Pamenepo Zofari wa ku Naama anayankha kuti

[2] “Kuvutika kwa mʼmaganizo kwanga kwandifulumiza kuti ndiyankhe chifukwa ndasautsidwa kwambiri.

[3] Ndikumva kudzudzula kondinyoza, ndipo kumvetsetsa kwanga kwa zinthu kwandifulumiza kuti ndiyankhe.

[4] “Ndithudi iwe ukudziwa momwe zinthu zakhala zikuchitikira kuyambira kale, kuchoka nthawi imene munthu analengedwa pa dziko lapansi,

[5] kuti chisangalalo cha woyipa nʼchosachedwa kutha, chimwemwe cha wosapembedza Mulungu nʼchakanthawi kochepa.

[6] Ngakhale atamayenda mapewa ake ali mmwamba ndipo mutu wake uli nengʼaa,

[7] iye adzatheratu monga momwe imatayikira ndowe yake yomwe; iwo amene ankamuona adzati, ‘Kodi uje uja ali kuti?’

[8] Adzazimirira ngati maloto ndipo sadzapezekanso, adzachotsedwa ngati masomphenya a usiku.

[9] Diso limene linamuona silidzamuonanso; sadzapezekanso pamalo pake.

[10] Ana ake adzabwezera zonse zimene iyeyo analanda anthu osauka;

[11] Mphamvu zaunyamata zimene zili mʼthupi mwake zidzagona naye limodzi mʼfumbi.

[12] “Ngakhale zoyipa zili zozuna mʼkamwa mwake ndipo amazibisa kunsi kwa lilime lake,

[13] ngakhale salola kuzilavula, ndipo amazisunga mʼkamwa mwake,

[14] koma chakudya chake chidzawawasa mʼmimba mwake; chidzasanduka ngati ndulu ya njoka mʼkati mwa iyeyo.

[15] Adzachisanza chuma chimene anachimeza; Mulungu adzachitulutsa mʼmimba mwa munthuyo.

[16] Iye adzayamwa ndulu ya njoka ndipo ululu wa mphiri udzamupha.

[17] Sadzasangalala ndi timitsinje, mitsinje yoyenda uchi ndi mafuta.

[18] Ayenera kubweza zimene anazigwirira ntchito osazidya; sadzasangalala ndi phindu la malonda ake.

[19] Pakuti iye anapondereza anthu osauka ndipo anawasiya wopanda thandizo; iyeyo analanda nyumba zimene sanamange.

[20] “Chifukwa choti umbombo wake sutha, sadzatha kusunga chilichonse chimene amakondwera nacho.

[21] Palibe chatsala kuti iye adye; chuma chake sichidzachedwa kutha.

[22] Ngakhale ndi munthu wachuma, mavuto adzamugwera; mavuto aakulu adzamugwera.

[23] Akadya nʼkukhuta, Mulungu adzamugwetsera ukali wamoto ngati mvula yosalekeza.

[24] Ngakhale athawe mkondo wachitsulo, muvi wamkuwa wosongoka udzamulasa.

[25] Muviwo adzawutulutsira ku msana, songa yake yowala kuchoka mʼmphafa mwake. Adzagwidwa ndi mantha aakulu;

[26] mdima wandiweyani ukudikira chuma chake. Moto wopanda wowukoleza udzamupsereza ndi kuwononga zonse zotsala mʼnyumba yake.

[27] Zamumlengalenga zidzawulula kulakwa kwake; dziko lapansi lidzamuwukira.

[28] Chigumula cha madzi chidzawononga nyumba yake, katundu wake adzatengedwa pa tsiku la ukali wa Mulungu.

[29] Izi ndi zimene Mulungu amasungira anthu oyipa, mphotho imene Mulungu amayikira iwowo.”

Yobu — Chapters